Kutonthoza Oferedwa

Chisilamu ndi njira yokwanira komanso yangwiro ya moyo yomwe yaganizira zosowa zonse za munthu. Sizinangosonyeza njira ya mtendere m’moyo wa munthu, komanso zasonyeza mmene tingasonyezere chikondi ndi mtendere munthu akamwalira. Choncho Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adausonyezera Ummah momwe ungatonthozere ndi kuwapepesa ofedwa amene ali m’masautso.

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene angatonthoze munthu amene ali m’masautso adzalandira malipiro ofanana ndi amene wafedwa (malipiro omwe amalandira namfedwa chifukwa chogwiritsa ntchito sabr pamavuto ake).

Mu Hadith ina, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe okhulupirira amene amatonthoza m’bale wake Msilamu nthawi yamavuto kupatura kuti Allah adzamumveka munthu ameneyo nkanjo wa ulemelero tsiku la Qiyaamah. (Sunan Al-Tirmidhi, No.: 1073)

Check Also

Kutonthoza Oferedwa

7. Nkoloredwa kuyamikira omwalirayo. Komabe, pomutamanda, onetsetsani kuti simukukokomeza kapena kumutamanda pa makharidwe amene panalibe …