Dua ya Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) Iyankhidwa

Nthawi ina, Arwa bint Uwais, neba wa Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu), adadza kwa Muhammad bin ‘Amr bin Hazm (Rahimahullah) ndi dandaulo lokhudza neba wake Hazrat Sa’eed bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu).

Ananena kuti adamanga khoma lake m’malo mwake ndipo adapempha Muhammad bin Amr (Rahimahullah) kuti apite kwa iye kuti akamuyankhulire m’malo mwake. Adatinso: “Ndikulumbira mwa Allah Ta’ala ngati Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) sandibwezera zomwe ndiyenera kuchita, ndilengeza poyera za chipongwe chimene wandichitira kwa anthu onse mu mzikiti wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).

Muhammad bin Amr bun Hazm (Rahimahullah) anamuchenjeza kuti: “Usamukhumudwitse mnzake wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayh wasallam) (pomunamizira Hazrat Sa’iyd bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu)) Si munthu amene angakupondereze kapena kukulanda ufulu”.

Atakhumudwa ndi yankho lake, Arwa adanyamuka napita kwa Umaarah bin Amr ndi Abdullah bin Salimah (Rahimahumallah), ndipo adawafotokozera awiriwa madando ake. Atamva pempho lake,awiriwa adapita kwa Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe adali m’malo mwake a Aqiq. Iye atawaona anawafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani mwabwera kuno? Adamufotokozera madandaulo a Arwa ndi pempho lake kwa iwo.

Hazrat Said bun Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha kuti: “Ndidamumva Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) akunena kuti: “Amene angalande chuma cha munthu aliyense ngakhale chitakhala chochuluka ngati Shibr (chokwana dzanja limodzi), adzabwera pa tsiku la Qiyaama ndi nthaka yomangidwa m’makosi ake asanu ndi awiri.”

Pambuyo pake adati: “Muloreni abwere kudzatenga malo anga omwe akudzinenera molakwika kuti ndi ake.” Ndipo adamutemberera nati: “E, Allah, ngati ali wabodza pa zomwe akundinenera ine, musamusiyesiye.

Adapemphanso kuti Allah Ta’ala alore kuti choonadi chionekere kwa Asilamu.

M’zitabu zina zanenedwa kuti Hazrat Said bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Ndikulumbira m’dzina la Allah Ta’ala, ndamupatsa kale ma ziraa mazana asanu ndi limodzi a chuma changa chifukwa chabodza limene wandinenera ine. Kenako adatchura Hadith yomwe yatchuridwa pamwambayi.

Pambuyo pake Arwa adadza kwa iye natenga gawo la nthaka yake yomwe adamangapo mpanda wake. Kenako anagwetsa linga limene iye anamanga n’kudzimangira nyumba pamalopo.

Patangopita nthawi yochepa, dera lonse la ‘Aqiiq linakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi komwe kunali kosayerekezeka komwe kudapangitsa kuti malire azinthu zonse ziwirizi azidziwika bwino. Inali nthawi imeneyo pamene zonena zake zabodza zidawulueika pamaso pa anthu ndipo chilungamo cha Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) chidaonekera kwa onse.

Patadutsa mwezi umodzi (chigumula chitatha), Arwa bint Uwais anasiya kuona ndipo anakhala wakhungu. Sipanapite nthawi yaitali, usiku wina akuyenda pa malo ake anagwera m’chitsime chake ndikufera momwemo. Mwanjira imeneyi matemberero a Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Arwa adakhala zenizeni.

Abu Bakr bun Muhammad bin Amr bin Hazm, m’modzi mwa osimba nkhani imeneyi, adati: “Pamene tinali achichepere, ndipo kukabuka mkangano pakati pa anthu awiri, nthawi zina tinkamumva munthu wina akuuza mnzake kuti, ‘Allah Taala akuchititse khungu monga momwe adammuchitira Arwa kukhala wa khungu. Tinkaganiza kuti mwina munthu wotukwanayo akunena za nyama yotchedwa Arwa (mbuzi ya mmapiri).

Check Also

Hazrat Sa’iid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) Apirira ku Mavuto Chifukwa Chachisilamu.

Hazrat Umar (radhwiyallahu ‘anhu) – munthu yemwe dzina lake loyera ndi njira yolemekezera chisilamu, ndipo …