1. Ta’ziat imatanthauza kugawana chisoni ndi ananfedwa ndi kuwamvera chisoni pa kutaika kwa okondedwa wawo. Izi zimachitika pomupangira dua omwalirayo pamaso pa akubanja ake. Momwemonso izi zidzachitika polipangira Dua banja lake, kupempha Allah Odalitsika ndi Wapamwambamwamba, kuti awadalitse powapatsa kupilira ku mayesero amenewa.
2. Dua ingachitike m’mawu awa:
“Allah amupatse omwalirayo (m’bale, tate, ndi ena otero) siteji yapamwamba kwambiri ku Jannah ndi kumukhululukira machimo ake,” ndiponso “Allah alipatse banja lake sabr-e-jamiil (kupirira kokongola).
3. Ndibwino kuti achibale (otalikirako monga azakhali a mayi ako) ndi abwenzi a omwalirayo awatonthoze achibale a omwalirayo. Komabe, malamulo a paradah (kusasakanikirana amuna ndi akazi) ayenera kutsatiridwa pakati pa amuna ndi akazi pa nthawi ya ta’ziyat.
4. Popanga ta’ziyat, onetsetsani kuti simukubweretsa chipsinjo kwa namfedwa.
5. Musaonjezere chisoni cha banjalo ponena mawu osayenera kapena kufunsa mafunso osayenera monga kufunsa achibale apamtima tsatanetsatane wa matenda omalizira kapena mamwaliridwe ake.