Kumuzindikiritsa Mwana Kwa Allah

Kulera mwana n’kofunika kwambiri ndipo tingakuyerekezere ndi maziko a nyumba. Ngati maziko a nyumba ali olimba, ndiye kuti nyumbayo idzakhalanso yolimba ndipo idzapirira ku nyengo iliyonse.

Mosiyana ndi zimenezi, ngati maziko a nyumbayo ndi ofooka komanso ogwedezekagwedezeka, ndiye kuti ndi kugwedezeka pang’ono, nyumbayo idzagwa.

Chimodzimodzinso, kulera mwana ndiko maziko amene moyo onse wa mwanayo wazikidwapo. Kuti mwana apite patsogolo ndi kutukuka pa tsogolo lake, mwanayo amafunikira kuleredwa bwino mwa Chisilamu.

Chifukwa, ngati kulera kolondola kwachisilamu sikunaperekedwe kwa mwana, ndipo zikhulupiriro zachisilamu ndi makhalidwe abwino sizinakhazikitsidwe mwa iye, ndiye kuti kuvulaza ndi kuonongeka kwa izi kudzapitirira kumaonekera m’moyo wake onse.

Mwanayo amakumana ndi zovuta m’moyo wake wapakhomo pake momwe angachitire ndi mkazi wake ndi ana ake. Adzakumana ndi mavuto m’moyo wake pa ubwenzi wake ndi ndi achibale, oyandikana nawo komanso anthu onse. Sadzadziwa kulemekeza ndi kupatulika kwa chipembedzo ndi kulemekeza ufulu wa anthu.

Mosapita kutali, chifukwa chosaphunzitsidwa dini yolondora ndikukuzidwa mwa Dini, sadzapita chitsogolo pa Dini yake komanso umoyo wake udzakhunzika kwambiri.

Ufulu wa Mwana pa Makolo

Kulera mwana mwa Chisilamu ndi ufulu wa mwanayo pa makolo ake. Zanenedwa kuti ma Swahaabah nthawi ina adamufunsa Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) kuti: “Oh Mtumiki wa Allah, tikudziwa ufulu wa bambo pa ana ake komano sitikudziwa ufulu wa mwana pa bambo ake!

Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) anayankha kuti: “Ufulu wa mwana pa bambo ake ndi kuti bambo ake amupatse dzina labwino ndikumuphunzitsa makhalidwe a Chisilamu.”

Zanenedwa kuti Olemekezeka Ibnu Umar Radhwiya-Allahu anhu nthawi ina adamulangiza munthu wina kuti: “Onetsetsani kuti mwana wanu akuleredwa bwino mwa Chisilamu, chifukwa mudzafunsidwa pa izi pa tsiku la Qiyaamah. Mudzafunsidwa za mtundu wa maphunziro omwe mudamupatsa ndi makharidwe omwe mudamupatsa, pomwe nayenso adzafunsidwa ngati adakumverani.”

Kupanga Azaan ndi Iqaamah M’makutu mwa Mwana Wakhanda

Mkatikati molera mwana, chinthu choyamba ndicho kumuthandiza kudziwa Allah Wamphamvuyonse. Choncho, tikuikira umboni kuti mwana akabadwa, ngakhale zaka zozindikira zisanafike, Shariya chimalamura kuti azaan iyitanidwe ku khutu lakumanja la mwana ndi iqaamah kukhutu lakumanzere kwa mwanayo.

Zonsezi zimachitika pofuna kuuumba mtima wa mwanayo ku Imaan ndi kukhanzikitsa umodzi ndi ukulu wa Allah mu mtima mwake. Mu kuyankhula kwina, atabwera padziko lapansi, chinthu choyamba chimene mwanayo amadziwitsidwa ndi Allah, Odalitsika ndi Wammwambamwamba.

Kuphunzitsa Mwana Makhalidwe Achisilamu

Mtumiki (Swallallaah Alaihi Wasallam) Kudzera mu zochita zake zodaritsika, adauphunzitsa Ummah kuti uphunzitse ana awo kutchula dzina la Allah Odaritsika ndi wapamwambamwamba nthawi ya chakudya. Choncho, mwanayo ayenera kumvetsa kuti chakudya chimene akusangalala nacho ndi chopatsidwa ndi Allah.

Hazrat Umar ibn Abi Salamah (Allah asangalale naye) anasimba kuti nthawi ina ali mwana, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) anamuuza kuti: “Yamba kudya potchula dzina la Allah. Dyera dzanja lamanja ndipo udzidya mbalj yako.”

Mu Hadith imeneyi, Mtumiki wa Allah (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) adapereka Sunnat zitatu kwa mwana wamng’onoyu, ndikumutsimikizira kuti ngakhale pamene tikudya tizikumbukira kukwaniritsa maufulu a Allah (wolemekezeka ndi wolemekezeka).

Kuonjezera apo, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adalangiza ndi kumuphunzitsa mwanayo mwachikondi ndi chifundo kotero kuti phunzirolo lidakhanzikika mumtima mwake. Choncho, akunena kuti kuyambira tsiku limenelo, nthawi zonse ankaonetsetsa kuti azichita zomwe Mtumiki wa Allah (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adamuphunzitsa.

Kuika Kufunika Kokwaniritsa Ufulu wa Allah mu Mtima wa Mwana

Pamene mwanayo akukula, Mtumiki wa Allah (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) adauphunzitsa Ummah kuti uyenera kukakamiza mwanayo kukwaniritsa malamulo a Allah,ndipo mwa malamulo onse a Allah lamulo lofunikira kwambiri ndi la Swalah.

Rasulullah (swallallahualaihiwasallam) adati: “Aphunzitseni ana anu kuswali akakwanitsa zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo apatseni chilango ngati akukana kuswali akakwanitsa zaka khumi.”

M’mawu ena, ngakhale kuti mwanayo ali wamng’ono, ndipo swalah siinakakamizidwe pa iye, tikulangizidwa kuti titsindike kwa mwanayo kufunikira kokwaniritsa ufulu waukulu wa Allah otchedwa swalah.

Momwemonso, chitsimikizo chokhudza ukulu opanda malire ndi mphamvu zopambana za Allah zikuyenera kukhazikitsidwa mu mtima mwa mwana kuyambira ali wamng’ono.

Mwanayo akuyenera kukula akuzindikira kuti Allah yekha ndiye gwero la zabwino zonse m’moyo wake, ndikuti palibenso ulemelero ndi mphamvu kupatula Allah.

Check Also

Ntendere Waukulu Wa Allah Pa Akapolo Ndi Kukhala Makolo

Ena mwa madaritso aukuluakulu a Mulungu pa munthu, ndi mdaritso okhala ndi makolo. Mwayi okhalandi …