7. Nkoloredwa kuyamikira omwalirayo. Komabe, pomutamanda, onetsetsani kuti simukukokomeza kapena kumutamanda pa makharidwe amene panalibe mwa iye. Momwemonso musatengere chikharidwe ndi njira za makafiri pomutamanda.
8. kuchuluka kwa nthawi ya ta’ziyat ndi masiku atatu kuchokera tsiku lomwalira. Pambuyo pa tsiku lachitatu, ndi makruh kupanga ta’ziyat. Komabe, ngati munthu sadathe kubwera ku ta’ziyat m’masiku atatu chifukwa cha ulendo omwe anali nawo, akadzabwerako ku ulendoko, akhonza kukapanga ta’ziyat ngakhale kuti masiku atatu adutsa.
9. Ndi makruh kwa munthu kubwerezanso kuchita ta’ziyat pomwe utachita kale.
10. Kwabwino kuchita ta’ziyat maliro ataikidwa m’manda. Komabe nkoloredwa kupanga ta’ziyat asanaikidwenso.
11. Ngati wina sangathe kudzionetsera kopanga ta’ziyat chifukwa cha zinthu zina, ndiye kuti akhonza kulemba kalata kapena kutumiza uthenga wachipepeso kubanja la omwalirayo.
12. Hazrat Rasulullah (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adatonthoza ofedwa ndi mawu awa:
إِنَّ لِلَّهِ مَا أَخَذَ وَلَهُ مَا أَعْطَى وَكُلٌّ إِلَى أَجَلٍ مُسَمًّى فَلْتَصْبِرْ وَلْتَحْتَسِبْ
Innaa lillah maa akhadha walahu maa a’twaa wakullun ilaa ajalin musamma faltasbir waltahtasib. Allah zomwe watenga ndi zomwe wapereka ndi zake ndipo chirichonse chili ndi nthawi yoikika, pilirani ndikukhala ndi chiyembekezo kwa Allah.