13. Sizoloredwa kupita ku nyumba ya kafiri yemwe wamwalira kukapepesa mwambo wamaliro uli mkati. Koma akakhala kuti ndi kafiri oyandikana naye nyumba kapena kaafir aliyense amene wataya wachibale wake, mwachitsanzo, mwana, ukhoza kumutonthoza ndi mawu awa:
أَخْلَفَ اللّه عَلَيْكَ خَيْرًا مِنْهُوَاَصْلَحَكَ
Akhlafa Allahu ‘Alayka Khayran Minhu Wa ‘Aslahaka
Allah akupatse zabwino (akudalitse ndi tawfiiq yolowa Chisilamu) posinthana ndi munthu amene mwatayayo, ndipo Allah akukonzereni chikhalidwe chanu.
14. Athandizeni oferedwa powatumizira chakudya kunyumba kwawo. Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adawaphunzitsa ma Swahaabah (Radhwiyallahu anhum) kuti azimva chisoni ndi ofedwa ndi kuwathandiza pa nthawi yolira ndi yachisoni chawo. Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adawalimbikitsa Maswahaabah (Radhwiyallahu anhum) kuti akonze chakudya ndikutumiza kubanja lawo, chifukwa ch zovuta zomwe zawapeza kudzawavuta kuti alongosore za zosowa zawo.
Olemekezeka Abdullah bin Ja’far radhwiyallahu anhu akufotokoza; nkhani ya kumwalira kwa Ja’far itafika (i.e kuphedwa kwake pa nkhondo ya Mu’tah) Rasululullah swallallahu alaihi asallam adati (kwa maswahabah radhwiyallahu anhum) likonzereni chakudya banja la Ja’far radhwiyallahu anhu, popeza chawapeza chipsinjo chomwe chawatanganidwitsa kuti asakwanitse kuzipezera zosowa zawo.[1]
15. Shari’ah sichidafotokoze mtundu uliwonse wa chovala kapena maonekedwe a chovala choti avale anamfedwa.[2]
16. Miyambo yoti alendo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri (7), tsiku la 10 ndi la 40 “Arbaini” ndi zina zotero ndi zopeka ndipo ziyenera kusiidwa.
17. Anamfedwa kukonzera Chakudya anthu omwe odzapepesa sizofunikira. Anamfedwa kupereka chakudya ndi zongopekedwa.
18. Ndizoletsedwa kulemba ganyu munthu kuti awerenge gawo la Qur’an ndi cholinga choti sawabu zipite kwa omwalirayo.
[1] عن عبد الله بن جعفر رضي الله عنه قال لما جاء نعي جعفر قال النبي صلى الله عليه وسلم إصنعوا لأهل جعفر طعاما فإنه قد جاءهم ما يشغلهم (سنن الترمذي، الرقم: 998، وقال: هذا حديث حسن)
[2] عن عائشة رضي الله عنها قالت قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من أحدث في أمرنا هذا ما ليس فيه فهو رد (صحيح البخاري، الرقم: 2697)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu