
M’nthawi ya khilaafah ya Olemekezeka Mu’aawiyah (Radhwiya Allahu ‘anhu) adalembera kalata Marwaan bin Hakam bwanamkubwa wake yemwe adasankhidwa ku Madinah Munawwarah pomwe adamulangiza kutenga bay’at (chikole cha chikhulupiriro) kwa anthu a ku Madinah Munawwarah m’malo mwa mwana wake, Yaziid bin Mu’aawiyah, yemwe adzakhale Khalifah m’malo mwake mwake. Mu’aawiyah (Radhwiyallahu ‘anhu) sadazindikire za zolakwika za mwana wake Yaziid, choncho adafuna kuti amusankhe kukhala mlowa m’malo wake pa udindo wa khilaafah.
Komabe, Marwaan adanyalanyaza langizoli. Munthu wina wa ku Syria yemwe adali ku Madinah Munawwarah panthawiyo adamufunsa Marwaan chifukwa chomwe ankachedwera kutsatira langizo la Mu’aawiyah (Radhwiyallahu ‘anhu). Marwaan adayankha nati: “Ndikudikira kuti Sa’iid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) abwere kaye ndikupereka chikole, popeza iye akutengedwa kuti ndi mtsogoleri wa anthu komanso olemekezeka kwambiri mwa anthu a ku Madinah Munawwarah. Ngati angapereke chikole Yazid, ndiye kuti anthu ena amutsatiranso.”
Kenako munthu wa ku Siriya uja anapempha kuti: “Bwanji undilore ndim’bweretse kuti adzapereke? Adapita ku nyumba ya Saiid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adamulamura kuti abwere kwa Marwaan ndikupereka chikole pamaso pa Yaziid.
Olemekezeka Said bun Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha: “Inu mukhoza kubwerera; ndibwera kudzakwaniritsa (ndikafuna).
Munthu wa ku Siriya uja anakwiya ndipo anadzudzula mwaukali kuti: “Pitani pompano mukapereke chikore chanu, apo ayi ndikudulani mutu!
Olemekezeka Sa’iid bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti: “Inu mukundiitana kuti ndipereke chikole changa kwa munthu amene ndidayambana naye kale chifukwa cha chisilamu.” Ndi mawu amenewa, adadzionetsera yekha kuti adali m’gulu la maswahaaba oyambirira a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), chifukwa choti iye ankazindikira kuti ndi ndani amene ali oyenerera kupereka chikole cha Imaan kwa iye ndi ndani yemwe ali osayenera, ndipo mosakaika, Yaziid anali osayenera kupatsidwa chikole.
Kenako munthu wa ku Syria uja adabwerera kwa Marwaan ndikumuuza zomwe zidachitika, ndipo Marwaan adamulangiza kuti atonthole ndipo asawauze anthu zomwe zidachitikazi.
Choncho Said (Radhwiya Allaahu ‘anhu) sadabwere kudzapereka chikole kwa Yazid, ndipo Marwaan adamusiya ndikuyamba kutenga bay’at m’malo mwa Yazid kwa anthu a ku Madina Munawwarah.
Patapita nthawi, mkazi olemekezeka wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), Olemekezeka Ummu Salmah (radhwiyallahu ‘anha), anamwalira. Adapereka wasiya kuti Swalaah yake ya Janazah apempheretse ndi Saiid bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu). Chifukwa cha kulosera kwake, Marwaan sadapite patsogolo kukaswalitsa Swalaah yake ya Janaazah.
Akudikira Said bun Zaid, munthu wa ku Syria uja adamufunsa Marwaan kuti: “Bwanji iwe sukupita patsogolo kukatsogolera Swalah ya Janaazah?”
Marwaan adayankha: “Ndikudikira munthu amene umafuna kumudula mutu (pamene samafuna kubwera kudzapereka chikole pamaso pa Yazid),” Marwaan adanena izi kunena Said bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu).
Munthu wa ku Syria uja atamva izi adazindikira kulemekezeka kwa Said ndipo nthawi yomweyo adapanga istighfaar, kupempha chikhululuko kwa Allah Taala pa zolakwa zomwe adamuchitira Saiid (Radhwiya-Allah anhu). (Tareekh Ibnu Asaakir 21/88, Mustadrak #5853 and Al-Mu’jamul Kabeer #345)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu