Salaam ndi moni wa Chisilamu. Monga momwe Chisilamu chimatanthauza mtendere, moni wa Chisilamu ndi moni wamtendere komanso ofalitsa uthenga wamtendere. Salaam ndi imodzi mwa zochitika zachisilamu zomwe ndi chizindikiro cha Msilamu, ndipo kufunika kwake kwatsindikitsidwa kwambiri mahadith.
Olemekezeka Abdullah bin Salaam (Radhwiyallahuanhu) akuti:
Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) atasamuka kupita ku Madina, anthu a mumzinda wa Madina adathamanga kukamulandira. Ndinamva wina akufuula kuti, “Mtumiki wa Mulungu wafika! Mtumiki wa Mulungu wafika! Mtumiki wa Mulungu wafika!”
Ndidatengana limodzi ndi anthu kuti ndikadzionere ndekha (munthu amene anthu ankati ndi mtumiki wa Allah, ngakhale kuti ine ndidali ndisanalowe Chisilamu kufikira pamenepo). Posakhalitsa maso anga adaona nkhope ya Rasulullah ndipo ndidakhulupirira kuti nkhope iyi siingakhale nkhope ya onyenga kapena wabodza.
Mawu oyamba amene ndinamumva akulankhula kwa anthu omwe adali m’nthawi yachisangalalo) adali: “E, inu anthu falitsani salaam pakati panu (mukakumana) adyetseni osowa, limbikitsani ubale, dzukirani pakati pa usiku kuswali pamene ena ali ntulo, kudzera mukuchita zimenezi mudzadalitsidwa pokalowetsedwa kh Jannah!
Mu Hadith yolemekezeka, Rasulullah adalongosola kuti kupanga salaam ndi njira yokhanzikitsira chikondi pakati pa anthu onse mu Ummah, komanso ndi njira yokalowera ku Jannah.
Rasulullah swallallah alaihi wasallam adati: “Simudzalowa ku Paradiso mpaka mutabweretsa Imaan, ndipo simungakhale ndi Imaan yokwanira mpaka mutakondana pakati panu. Kodi ndisakusonyezeni njira yolimbikitsira chikondi pakati panu? Pangani salaamu kukhala chizolowezi chanu pakati panu ( mukakumana).”
Kupereka moni kwa Msilamu ndi umodzi mwa maufulu asanu ndi umodzi omwe munthu aliyense ali nawo pa m’bale wake wachisilamu.
Munthu akamlonjera m’bale wake wa Chisilamu ndi salaamu, amamuchitira zabwino m’njira zitatu:
1) Amamuchitira dua kuti Allah amukhanzike mwamtendere, as salaam ndi malonje amtendere.
2) Amamukumbutsa kuti Allah ali naye ndi kumuyang’anira nthawi zonse, pakuti ‘Salaam’ ndi dzina la Allah.
3) Akumuuza kuti akamlonjera ndi salaam, ndithu, iye wamufunira zabwino ndipo sadzamuchitira choipa chilichonse (chomuyankhulira, ngakhale chathupi kapena mwa njira ina iliyonse).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu