Ubwino Oyambilira kupanga Salaam
Olemekezeka Abdullah bun Masuud (Allah asangalale naye) akusimba kuti Rasulullah (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) adati: “Amene amayambilira kupereka Salaam ndi osadzitukumura.”[1]
Njira Yokhanzikitsira Chikondi
Olemekezeka Abu Hurairah (Allah asangalare naye) akusimba kuti Rasulullah (madalitso ndi mtendere zipite kwa iye) adati: “Simudzalowa ku Paradiso pokhapokha mutakhulupilira, ndipo simungakhale okhulupilira kwenikweni kufikira mutakondana pakati panu?[2]
Ntchito Yapamwamba Mchisilamu
Olemekezeka Abdullah bin Amr (Allah asangalale naye) akunena kuti munthu wina adamufunsa Rasulullah (madaritso ndi mtendere zipite kwa iye) kuti: “Ndi chikharidwe chanji ndi nchitidwe wa Chisilamu zomwe zili zoyamikirika ndi zabwino?” Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) adati: “Kudyetsa zolengedwa ndi kupereka moni wachisilanu (kupereka salaam) kwa anthu, kaya mukuwadziwa kapena ayi.”[3]
Imabweretsa Madalitso Mnyumba
Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) adati: Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) nthawi ina adandiuza: “E, iwe mwana wanga okondedwa! Ukalowa m’nyumba mwako, upereke salamu ku banja lako. Iyi ndi njira yopezera madaritso kwa iwe ndi banja lako.[4]
[1] شعب الإيمان للبيهقي، الرقم: 8407، وقال المناوي في فيض القدير، الرقم: 3191، وفيه أبو الأحوص قال ابن معين: ليس بشيء وأورده الذهبي في الضعفاء
[2] صحيح مسلم، الرقم: 54
[3] صحيح البخاري ، الرقم: 12
[4] سنن الترمذي، الرقم: 2698، وقال: هذا حديث حسن غريب
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu