
Zanenedwa kuti nthawi ina munthu wina adadza kwa olemekezeka Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu anhu) nati: “Ndili ndi chikondi chachikulu pa Ali (Radhwiya-Allahu ‘anhu) mu mtima mwanga moti sindikonda china chilichonse monga momwe ndimamukondera.” Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu ‘anhu) adamuyamikira iye chifukwa cha chikondi ndi ulemu wake kwa Ali (Radhwiyallahu ‘anhu) nati: “Izi nzabwino kwambiri! Muli ndi chikondi mu mtima mwanu pa munthu yemwe ali ochokera ku Jannah (chifukwa Ali (Radhwiya-Allahu anhu) adapatsidwa nkhani yabwino ya Jannah adakali pa dziko pompano kudzera kwa Mtumiki wa Allah SwallaAllaahualayhiwasallam).
Munthuyu pambuyo pake adati: “Ine ndili ndi chidani mu mtima mwanga cha Uthmaan (Radhwiya-Allahu ‘anhu) kotero kuti sindidana ndi china chilichonse ngati momwe ndimamudera iye.” Said bun Zaid (Radhwiya-Allaahu ‘anhu) adamuuza kuti: “Wachita zoipa ndi zolakwa kumuda Uthmaan (Radhwiya-Allahu ‘anhu) dziwa bwino kuti mumtima mwako uli ndi chidani cha munthu amene ali waku Jannah (popeza Uthmaan (Radhwiya-Allahu anhu) adaizidwa zokalowa ku Jannah adakali pa dziko lapansi pompano).
Sa’iid bin Zaid (Radhwiya-Allahu ‘anhu) anasimba Hadith ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) nati: “Nthawi ina Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adakwera phiri la Hiraa pamodzi ndi Abu Bakr, Umar, Uthmaan,Aliyy,Talha ndi Zubair. Radhwiya-Allah ‘anhum) Phiri lidayamba kunjenjemera ndi kugwedezeka (chifukwa cha chisangalalo powona kuti anthu akuluakuluwa aima pamenepo).
“Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adaliyankhula phirilo nati: “Khanzikika, iwe Hiraa, popeza pa iwe pali Nabiy, Siddiiq ndi shahiid.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu