Kuonongeka kwa Ummah asadafike Dajjaal

Zatchuridwa mMahadith kuti Qiyaamah isanafike, khumbo lalikulu la anthu lidzakhala kudzikundikira ndi kusonkhanitsa chuma. Anthu adzachitenga chuma ngati mfungulo ya zinthu zonse zapamwamba ndi chitonthozo, khomo la zosangalatsa zamtundu uliwonse ndi zansangulutso, ndi chida chokwaniritsira zokondweretsa za thupi ndi zilakolako za dziko. Kotero, adzapereka chilichonse kuti apeze ndipo adzachita chilichonse kuti apeze.

Chilakolako chonyanyira pa chuma chidzawaononga ndi kuwapangitsa kukhala osasamala ndi kusawerengera za udindo wawo pa dini. Pofuna chuma, iwo adzakhala opanda chinyengo m’zochita zawo ndi kunyozera zikhalidwe zawo za dini. Ngakhale atakakamizidwa kuphwanya malamulo a shariah, pofuna kungofuna kupeza chuma chochuluka.

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Posachedwapa nthawi idzawadzera anthu pomwe munthu sadzakhala ndi nkhawa ndi chuma chimene wapeza, kaya chikuchokera mnjira ya halaal kapena haraam.” (Swahiyh Bukhaariy #2059)

M’ Hadith ina yanenedwa kuti Qiyaamah isanafike, chifukwa chokonda chuma, anthu adzakhala okonzeka kugulitsa dini yawo posinthanitsa ndi chuma chochepa chapadziko lapansi.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Fulumirani kuchita zabwino mafitnah asadayambe omwe adzakhale ngati magawo a usiku wa mdima. Munthu adzakhala okhulupirira m’bandakucha ndi kukhala kafiri madzulo, kapena madzulo adzakhala okhulupirira ndi kukhala kafiri pofika m’bandakucha. (Saheeh Muslim #118)

Munthu akaunika mavuto omwe Asilamu akukumana nawo masiku ano ndi mavuto osiyanasiyana omwe ummah ukukumana nawo, adzazindikira kuti akufanana ndi mayesero omwe afotokozedwa muhadith yomwe tafotokozayi. M’ Hadith zanenedwa kuti Dajjaal akadzatulukira, adzagwiritsa ntchito chuma chimenechi kusocheretsera anthu.

Chiwembu cha Dajjaal ndi Omuthandizira Ake

Zaka zingapo zapitazo, Aalim wina ankapita ku Bosnia kukagwira ntchito yothandiza anthu. Ali mu ndege, anakhala pafupi ndi Myuda wina. Mkatikati mwa ulendo wawo, anayamba kukambinara za chipembedzo. Aalim uyu anadabwa kwambiri Myudayo akumuuza kuti, “Taphunzira chipembedzo chanu cha Chisilamu ndipo taphunziranso Qur’aan ndi Hadith. Mwinanso timadziwa chipembedzo chanu kuposa inu.”

Myudayo pambuyo pake anati, “Titaphunzira chipembedzo chanu, tinafika potsimikiza kuti inu Asilamu muli ndi thandizo la uzimu la Allah Ta’ala, ndipo ndichifukwa chake Ayuda sanakwanitse kukugonjetsani kwathunthu. Komabe, tinaphunzira malemba anu kuti tipeze zofooka zanu ndi zinthu zomwe zingakuchotsereni thandizo la uzimu la Allah Ta’ala. Titaphunzira malemba anu, tinapeza kuti tiyenera kuchita zinthu zinayi zokha kuti mutaye thandizo la Allah Ta’ala.” Kenako Myudayo anatchula zinthu zinayi izi kwa Aalim:

  1. Tiyenera kulowetsa Asilamu mu masewera ndi mitundu ina yonse ya zasangulutso zomwe zingamawachotsere chidwi ndi kunyalanyaza maudindo awo a Deeni ndi udindo wawo kwa Allah Ta‘ala.
  2.  Tiyenera kuchotsa akazi achisilamu m’nyumba zawo ndikuwaika m’malo osiyanasiyana adziko lapansi. Ayenera kuyanjana ndi amuna achilendo ndikuchita nawo ntchito zonse zonyansa zomwe zidzawachotsere Hayaa ndi kudzichepetsa kwawo.
  3. Tiyenera kuwamiza mu riba (katapila) ndi chiwongola dzanja. Pochita izi, tidzachita zonse zomwe tingathe powapangitsa kukhala akapolo a mabanki ndi kukodwa mu machitidwe a mabanki, kotero kuwamiza mu katapira ndi chiwongola dzanja.
  4. Pomaliza, tifunika kubweretsa kusamvana pakati pa Asilamu. Tidzafunafuna njira zomwe tingapangire kuti anthu ambiri achoke ku Ulama -e-Haqq ndikutaya chidaliro mwa iwo. Izi zidzapangitsa kuti munthu aliyense atsate njira yake ndikutengera Deen m’manja mwake. Zotsatira zomvetsa chisoni za izi sizidzakhala kanthu koma kusokonekera kwathunthu kwa Deen m’miyoyo ya Asilamu.

Atanena izi, Myudayo adanenanso kuti dongosolo lomwe adakhazikitsa lidapambana. Ichi ndichifukwa chake tikupeza kuti ummah wachisilamu wachoka kutali ndi Deen ndipo thandizo la Allah Ta’ala likuchoka kwa iwo.

Tikamaona dongosolo lomwe Ayuda adakhazikitsa pofuna kusocheretsa ummah, tipeza kuti Dajjaal akadzawonekera, adzagwiritsa ntchito dongosolo lomweli (akazi, chuma ndi zasangulutso) kuti awalande anthu Imaan yawo ndikuwalanda Deen yawo.

Check Also

Zizindkiro za Qiyaamah 5

Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah pa nkhani ya Dajjaal Kutulukira komanso kubwera kwa ma …