1. Ukakumana ndi Msilamu nzako, mupatse salaamu.
Olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu akunena kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Msilamu ali ndi ma ufulu asanu ndi umodzi pa Msilamu nzake. Akakumana naye amlonjere (ndi salamu); ngati amuitana avomere kuitana kwake; akayetsemula amupangire duwa ponena kuti. ‘Yarhamukallah’ akadwala azikamuona akamwalira aziperekeza nawo janaazah yake;
2. Rasulullah swallallah alaihi wasallam adatilimbikitsa kudzera mmahadith kupereka salaam pakati pathu. Kupanga salaam kudzakhala njira yolimbikitsira chikondi ndi umodzi pakati pathu.
Abu Hurairah radhwiyallahu anhu akusimba kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasalllam adati: “Simudzalowa ku Paradiso mpaka mutabweretsa Imaan, ndipo simudzakhala ndi Imaan yangwiro kufikira mutakondana pakati panu. Kupangeni kupereka salaam kukhala Chizoloŵezi mwa inu nokha (i.e. pamene nwakumana wina ndi mzake). “
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu