
Tsiku lina Abdullah bin Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) akukonzekera kupita ku Swalaah, adamva kuti amalume ake, Sa’iid bin Zaid (radhiyallahu ‘anhu) akudwala kwambiri ndipo atha kumwalira.
Nkhaniyi idamufika pa nthawi yomwe adali atadzola kale (mafuta onunkhiritsa) thupi lake ndipo ali pafupi kuchoka kwawo kupita ku Swalaah ya Jumuah.
Koma atamva nkhani imeneyi, nthawi yomweyo adakwera chifuyo chake ndipo m’malo mopita ku Jumuah, adauyamba ulendo opita ku Aqeeq, komwe kunkakhala Said (Radhwiyallahu ‘anhu). Aqeeq anali malo akutali ndi tawuni, komwe Swalaah ya Jumuah siinali yokakamizidwa kwa anthu okhala kumeneko, popeza zoyenereza za Swala ya Jumah zidali zisadapezeke.
Abdullah bin Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) adapita ku Aqeeq ndikukathandiza kusambitsa thupi la Sa’iid (radhwiyallahu ‘anhu). Atamusambitsa, adamuveka kafani (sanda) ndipo adaswalira nawo janaazah limodzi ndi anthu ena.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu