3. Njira ya Sunnat yakaperekedwe ka salaam ndi kupereka moni kwa Asilamu onse, osati achibale ake, abwenzi ake ndi amene akuwadziwa okha.
Olemekezeka Abdullah bin Amr radhwiyallahu anhu akusimba kuti munthu wina adamufunsa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam “Kodi ndi chikhalidwe chanji ndi mChisilamu chomwe chili choyamikirika komanso chabwino?” Adayankha Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam: “Kudyetsa zolengedwa ndi kupereka salaamu kwa anthu, kaya ukumudziwa kapena ayi.”
4. Upereke salaamu ponena kuti “Assalaamu alaikum.” Mukhozanso kupereka salaamu ponena kuti “Assalaamu alaikum wa rahmatullah” kapena “Assalaamu alaikum wa rahmatullahi wa barakaatuhu”. Mukapereka salaamu yayitali, mudzalandira mphotho yochulukirako.
Olemekezeka Imraan bun Husain radhwiyallahu anhu akusimba kuti munthu wina adadza kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam namulonjera kuti: “Assalaamu alaikum.” Adayankha Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam salaamu ndipo munthuyo adakhala nawo pagulupo. Kenako Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Walandira malipiro khumi.” Pambuyo pake, munthu wina anabwera kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam ndipo adamlonjera kuti: “Assalaamu alaikum wa rahmatullah.” Nabi swallallahu alaihi wasallam adayankha salaamu ndipo munthuyo adakhala pagulupo. Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Walandira malipiro makumi awiri.” Kenako munthu wina adadza kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam namulonjera kuti: “Assalaamu alaikum wa rahmatullahi wa barakaatuh.” Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adamuyankha salaamu ndipo munthuyo adakhala pansi. Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Iye walandira Malipiro makumi atatu.
5. Msilamu akakulonjera ndi salaamu, kudzakakamizidwa kwa iwe kuyankha salaamu, pokhapokha ngati uli ndi chowiringula chovomerezeka mwachitsanzo. Mukudya, mukuwerenga Quraan Majiid ndi zina zotero. Ngakhale sikuli kokakamizika kwa inu kuyankha salaamu pazimenezi, ndikoloredwa kuyankha.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu