
Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adakhala pansi ndi mwana wake Abdullah bun Umar, msuweni wake, Said bun Zaid, ndi Abbaas (radhwiyallahu ‘anhum). Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adawauza kuti: “Ndaganiza kuti sindidzaika munthu wina aliyense kukhala Khalifah pambuyo panga.”
Olemekezeka Sa’iid bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) pokhudzika za ubwino wa Asilamu ndi nkhani ya khilaafah, adayankha nati: “Mwina ngati mutaunikira za munthu wina mwa Asilamu yemwe ali oyenera paudindowu wa ukhilafah, ndiye kuti anthu atha kumudalira pa u khalifa (ndipo angathe kumuika kukhala) pambuyo pake.” Adatinso kwa Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adasankha khalifah asanamwalire ndipo anthu adadalira chisankho chake.
Poyankha izi Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati kwa iye: “Ndaona kuti anthu ena akungoyembekezera molakwika ndi kufuna kuti apatsidwe u Khalifa. Choncho, ndaganiza zoipereka nkhani imeneyi kwa anthu asanu ndi mmodzi ndikuwalora kuti asankhe munthu m’modzi mwa iwo kukhala Khalifa. Chifukwa chomwe chandipangitsa kuti ndisankhe anthu asanu ndi mmodzi amenewa ndi kuti ndi omwe ankawasankha (Mtumiki) ndipo adali okondwera nawo kwambiri pamene ankamwalira (pamene ankachoka padziko lapansi).
Maswahaaba asanu ndi m’modziwa anali: Olemekezeka Uthmaan, Ali, Zubair, Sa’d bun Abi Waqqaas, Talhah bun Ubaidullah ndi Abdur Rahmaan bun Auf (radhwiyallahu ‘anhum).
Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adanenanso kuti: “Mwa anthu awiriwa m!modzj akanakhala kutj adakal moyo pamopa, ndipo ndidamsankha mmodzi mwa iwo kukhala Khalifa pambuyo panga, ndikadakhala ndi chidaliro chonse (mwa iye kukhala oyenerera ukhilafah). Anthu awiriwa ndi Saalim (Radhiyallahu ‘anhu),kapolo omasuridwa
kapolo wa Abu Huzaifah (Radhwiyallahu ‘anhu), ndi Abu Ubaidah bin Jarraah (radhiyallahu ‘anhu).”
Anthu awiriwa adamwalira mu nthawi ya khilaafh ya Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu). (Musnad Ahmad #129)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu