Mu kulera mwana, ndi zofunika kwambiri kuti makolo azionetsetsa kuti mwana wawo nthawi zonse apezeka m’gulu la anthu ochita zabwino ndipo ndikupezeka malo abwino.
Malo abwino komanso anthu opembedza adzasiya chikoka chokhanzikika pamtima wa mwanayo zomwe pambuyo pake zidzaumba kaganizidwe kake ndi kawonedwe kake ka moyo.
Zotsatira zake, mwanayo adzakula ndi maganizo oyenera a Chisilamu ndipo mtima wake udzaumbidwa ndi mfundo zenizeni za Chisilamu.
Hadith ikufotokoza kuti mwana aliyense amabadwa ali ndi khalidwe loyera. Makhalidwe amenewa adzamuthandiza kuona ndi kumvetsa choonadi cha Chisilamu pamene akukula. Komabe, kupyolera mwa mwanayo kukhala m’malo olakwika, mwanayo amasokonezedwa ndikuloŵa m’chipembedzo cholakwa. Choncho, mwana obadwira m’nyumba ya Myuda, Mkristu, kapena opembedza moto amatengera chipembedzo cha makolo ake.
Ubwino ndi Kuipa Kopezeka Mgulu la Anthu Abwino ndi Oyipa
Mu Hadith, Mtumiki (Swallallahualaihiwasallam) adamufanizira munthu owopa Allah ndi munthu onyamura pelefyumu, ndipo adamufanizira munthu oipa ndi munthu okweleza moto.
Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anafotokoza kuti ukamacheza ndi munthu onyamula pelefyumu, ngakhale kuti munthuyo sapatsidwako pelefyumu ngati mphatso kapena kugula kwa iye, ndiye kuti adzapindura ndi fungo lokoma la pelefyumu uku ali limodzi ndi iye.
Mosiyana ndi zimenezi, pocheza ndi munthu amene akukweleza moto, ngakhale chovala chake chisapse ndi moto, munthu adzakhudzidwabe ndi motowo kudzera ku fungo losasangalatsa la utsiwo.
M’ Hadith imeneyi, Mtumiki (Swallallahu alaiji wasallam) akufotokoza kuti kukhala pa ubwenzi wabwino sikudzakhala kopanda phindu, pamene kukhala m’gulu loipa sipadzalephera kukhala ndi vuto.
Tikamaphunzira za moyo wa maSwahaabah radhwiyallahu anhum timapeza kuti ankazindikira mwakuya zomwe ubwenzi wa munthu ndi anthu oyanjana ake amakhala nazo pa iye. Choncho, pali zambiri zomwe zimasonyeza nkhawa imene ma Swahaabah radhwiyallah anhum anali nayo pa ana awo kuti nthawi zonse azikhala limodzi ndi anthu abwino ndi oopa Mulungu.
Mmusimu muli nkhani ziwiri zomwe zikulongosora chikumbuntima chomwe ma swahaabah ankakhala nacho pa ana awo kuonetsetsa kuti adzipezeka mgulu la anthu ochita zabwino.
Kukhudzika Kwa Ummu Sulaim radhwiyallahu anha Pa Mwana Wake.
Zanenedwa kuti nthawiyo Mtumiki swallallahu alaihi wasallam atasamukira ku Madina Munawwarah, Hazrat Anas radhwiyallahu anhu anali wachichepere wa zaka zisanu ndi zitatu zokha. Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam atabwera amayi ake adamugwira dzanja lake napita naye kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam.
Atafika kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam Mayi wa Hazrat Anas radhwiyallahu anhu Adalankhula ndi Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam nati : Palibe mwamuna kapena mkazi wachi Answaar amene sadakupatseni mphatso; Komabe ndiribe choti ndingakupatseni ngati mphatso kupatula mwana wanga yekha basi, chonde mulandireni kuti azikutumikirani.
Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adavomera za kumutumikira kwake, ndipo adakhala ndi Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam kwa zaka khumi (10).
Mayi wa Hazrat Anas radhwiyallahu anhu Hazrat Ummu Sulaim radhwiyallahu anha ankadziwa ubwino okhala ndi anthu abwino. Popeza sipangakhale gulu labwino loposa kukhala ndi Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam, adafunitsitsa kuti mwana wake akapezeke kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam.
Olemekezeka Abbaas radhwiyallahu anhu akhudzika ndi Mwana Wake.
Olemekezeka Abbaas radhwiyallahuanhu, amalume ake a Mtumiki swallallahu alaihi wasallam ankafuna kuti mwana wake Abdullah bin Abbaas apeze madalitso apadera pokhala m’gulu lodalitsika la Rasulullah swallallahu alaihi wasallam,Choncho, zanenedwa kuchokera kwa Abdullah bin Abbaas kuti ali mnyamata wa zaka khumi ndi ziwiri kapena khumi ndi zitatu, bambo ake Abbaas radhwiyallahu anhu adamuuza kuti akagone ku nyumba ya azakhali ake Olemekezeka Maimunah radhwiyallah anha kuti akapindule kuchokera kwa Rasulullah swallallahu alaihi wasallam ndikuonetsetsa swalah yake ya Tahajjud.
Choncho Ibnu Abbaas radhwiyallahu anhu adakhala usiku onse ku nyumba ya azakhali ake, uku akuonetsetsa Swala ya Tahajjud ya Mtumiki swallallahu alaihi wasallam ndipo pamapeto pake adauphunzitsa ummah mmene Mtumiki swallallahu alaihi wasallam ankapemphelera swalah yake ya Tahajjud.
Kucheza sikuli pongocheza ku thupi kokha
Anthu akamaganizira za anthu ocheza nawo, nthawi zambiri amaganizira za abwenzi aku thupi okha. Komabe, mawu oti ‘abwenzi’ ndi ‘mgwirizano’ ali ndi tanthauzo lalikulu. Kwenikweni, chinthu chilichonse m’chilengedwe chimene chimakhudza kaganizidwe ka munthu, zimaumba maganizo a munthu ndipo zimakhudza khalidwe lake zikhoza kutengedwa ngati bwenzi kapena nzake.
Kotero, zolemba zomwe munthu amawerenga, mawebusayiti omwe amasakatula, ma akaunti a anthu ocheza nawo a pa Intaneti omwe amawatsatira, ndi zina zotero – zonsezi ndi mitundu yosiyanasiyana ya abwenzi omwe amaumba malingaliro ake ndi chikoka ndikusintha malingaliro ake potengera ndi zolinga ndi zochita zake pamoyo.
Kotero, monga momwe kuliri kofunika kwa makolo kukhala osamala ndi ozindikira ponena za abwenzi a ana awo, kuli kofunika momwemo kwa iwo kuyang’anira ndi kuongolera mbali zina za gulu zimene ana awo amakumana nazo.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu