6.Ziri Makruhu kupereka salaam kwa munghu yemwe watangwanika ndi ntchito ina ya Dini kapena akudya.
7. Musapereke salaam kwa omwe sali Mahram (Siwachibale). Ngati mkazi yemwe sali Mahram wapereka salaamu kwa mwamuna, koma kuti okalamba, ndipo palibe kuopa fitnah, akhonza kuyankhidwa. Komabe, ngati ndi mtsikana akupanga salaam, ndiye kuti munthu sayenera kuyankha ndi mawu. M’malo mwake akhoza kuyankha salaamu chamumtima.
8. Poyankha salaamu, zikuloledwa kuyankha ndi salaamu yofanana ndi mmene munalandilira. Komabe, mukayankha ndi salaam yayitali zidzakhala bwino komanso zopindulitsa. Mwachitsanzo, ngati mudapatsidwa salaam ndi mawu oti “Assalaamu alaikum”, mutha kuyankha kuti “Wa alaikumus salaam”. Komabe, ndibwino komanso zopinduritsa kwa inu kunena kuti “Wa alaikumus salaam wa rahmatullah” kapena “Wa alaikumus salaam wa rahmatullahi wa barakaatuhu.”
Allah akutchula m’Qur’an Majiid kuti: “Ndipo mukapatsidwa malonje, perekani malonje abwino kuposa ilo, kapena bwezani (monga momwemo).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu