
Olemekezeka Saiid bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) atamwalira, Hazrat Sa’d bun Abi Waqqaas (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Hazrat Abdullah bun Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) adali m’gulu la anthu omwe adasambitsa thupi lake.
Mwambo osambitsa utatha Jenezah idanyamuridwa ndi anthu ochokera ku Aqeeq kupita nayo ku Madina Munawwarah kuti akaikidwe ku manda otchedwa Baqi’ omwe akupezekera ku Madina Munawwarah, ikudutsa pa nyumba ya Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), iye (Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’nyumba mwake kuti akasambe mwachangu asadapite nawo kumanda.
Asanachoke kunyumba kwawo adalankhula ndi banja lake ndipo adati: “Sindinasambe chifukwa ndidasambitsa nawo thupi la Sa’iid (radhwiyallahu ‘anhu) ndangosamba chifukwa cha kutentha.” (Majmauz Zawaaid, #14880)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu