Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 4

9. Mawu a salaam amathera ndi “Wa barakaatuhu”. Munthu asawonjezere mau ena pambuyo pa “Wa barakaatuhu”

Muhammad bin Amr bin Ataa rahimahu-Allah adanena kuti: Nthawi ina ndidali chikhalire ndi Abdullah bin Abbaas radhwiyallahu anhu pamene munthu wina ochokera ku Yemen adafika pamalopa ndipo adapereka salaam kuti: “Assalaamu alaikum wa rahmatullahi wa baraakatuhu.” ndipo kenaka anaonjezera mau ku salaam. Nthawi imeneyo Abdullah bin Abbaas adali atasiya kuona, choncho adafunsa kuti: “Ndani ameneyu?” Anthu omwe adali pamenepo  adati: “Uyu ndi munthu wa ku Yemen amene amabwera ku misonkhano yanu. Adamufotokoza munthuyo mpaka Abdullah bin Abbaas radhwiyallahu anhu adamuzindikira. Abdullah bin Abbaas adati: “Salaam imathera ndi barakah (i.e. kutanthauza kuti baraakatuhu).”

10. Poyankha Salaam ya wina wake yankhani motulutsa mawu osati kungoimika dzanja kapena kugwedeza chabe mutu.

11. Gulu la anthu likakumana ndi munthu, ndipo m’modzi wa m’gululo akamuchitira salaam, ndiye kuti salaamu yake idzakwanira gulu lonselo. Momwemonso ngati munthu akumana ndi gulu la anthu ndikuwalonjera ndi salaam,munthu m’modzi wa gululo adzakwanira m’malo mwa gulu lonse.

Olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu akuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: “Pamene gulu la anthu likudutsana ndi munthu, zidzakwanira onse ngati mmodzi wa iwo apereka salaamu (kwa munthu amene akumana naye), ndipo gulu la anthu likakhala pansi, zimawakwanira onse ngati mmodzi mwa iwo ayankha salaamu (ya munthu amene wawalonjera).

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …