Kukhanzikika kwa Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Chisilamu

Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Sahaabi otchuka pakati pa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum), ndipo anali muazzin wa mzikiti wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam). Poyamba, iye anali kapolo wa ku Abyssinia wa osakhulupirira ku Makkah Mukarramah. Kutembenuka kwake kukhala Msilamu sikunali kokondedwa ndi bwana wake, kotero adazunzidwa mopanda chifundo.

Umayyah bin Khalaf, yemwe adali mdani oipitsitsa wa Chisilamu, ankamugoneka pa mchenga otentha masanasana ndipo ankamuika mwala olemera pachifuwa chake moti samatha ngakhale kusuntha chiwalo. Kenako amamuuza kuti: “Usiye Chisilamu, kapena ufe.

Ngakhale amakumana ndi masautso amenewa, Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) ankati: “Ahad! (Allah Mmodzi!) Ahad!

Usiku, ankamangidwa unyolo ndi kukwapulidwa, ndipo ankavulazidwa, ankagonekedwa pamalo otentha masana kuti asiye Chisilamu kapena kufa imfa yowawa chifukwa cha mabala. Ozunzawo ankatopa ndipo ankasinthanasinthana. Nthawi zina Abu Jahl ankamuzunza, pomwe nthawi zina Umayyah kapena munthu wina amamulanga, ndipo ankakangana wina ndi mzake pomuzunza chilango chowawa kwambiri, koma Hazrat Bilaal (Radhiyallahu ‘anhu) sankagonja.

Poona mazunzo aakulu omwe Hazrat Bilaal (Radhiyallahu ‘anhu) akukumana nawo, Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adagula ufulu wake, ndipo adakhala Msilamu omasuka.

Monga Chisilamu chinkaphunzitsa mosabisa za umodzi wa Mlengi wamphamvu zonse, pamene opembedza mafano a ku Makka Mukarramah ankakhulupirira mwa milungu yambiri ndi yaikazi, choncho Hazrat Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) ankangobwereza kuti: “Ahad! (Allah Mmodzi!) Ahad! (Al Isaabah 1/456, Fazaa’il-e-A’maal [Chingerezi] p. 21-22, [Urdu] p. 16-17)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …