12. Pangani salaam polowa m’nyumba. Ngati m’nyumba mulibe aliyense, muyenera kupereka salaamu ponena kuti:
السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللَّهِ الصَّالِحِينَ
Mtendere ukhale pa ife ndi pa akapolo abwino a Allah.
Olemekezeka Anas radhwiyallahu anhu adati: nthawi ina Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adandiuza kuti: “E iwe mwana wanga okondedwa,ukamalowa m’nyumba mwako, pereka salaam kwa akubanja ako anthu omwe ali mnyumba). Imeneyi idzakhala njira yopezera madalitso kwa iweyo ndi banja lako.”
13. Pochoka panyumba, chokani pakhomo ndi salaamu.
Hazrat Qataadah rahimahu-Allah akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Mukamalowa m’nyumba, perekani salaamu kwa omwe ali m’menemo, ndipo mukamatulukamo (m’nyumbamo), tulukani ndi salaamu kukhala chosungitsa chanu kwa anthu a m’nyumbamo (perekani salaam kwa anthu mukamatuluka mnyumba)
Zindikirani: Hazrat Nabiy swallallahu alaihi wasallam watiphunzitsa kupereka salaamu pochoka pakhomo ndipo adati: “Isiye salaamu yako ikhale chosungitsa kwa anthu apakhomo”. Nthawi zambiri, munthu akasunga zinthu zimene munthu wina wamudalira, amabwereranso m’tsogolo kuti akalandire. Choncho, munthu akachoka pachikhulupiriro cha salaam ndi anthu apakhomo, amakhala ngati akutenga mwayi ndikuika chiyembekezo chake pa chifundo cha Allah kuti Allah amubwezera kunyumba yomwe akutuluka.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu