30. Popanga musaafah, ingogwirani manja a munthuyo, Palibe chifukwa chogwirana chanza ndikumavinitsa monga amachitira ma kuffaar. Chimodzimodzinso sizoyenera kupanga musaafahah uku ndikumapsopsona dzanja lake ndikumasisita pachifuwa chake popeza machitidwewa alibe maziko mu Dini. 31. Popanga musaafah, musagwire manja a munthu winayo momufinya mpaka kumupweteka. 32. Musafulumire kuchotsa manja anu mukapanga …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 9
27. Wina asapereke salaamu pomlonjera munthu amene si Msilamu. Ngati amene sali Msilamu apereka moni wa salaamu, ayankhe pongonena kuti “Wa alaik” (ndi pa inu), ndipo ngati ambiri omwe si Asilamu apereka salaam kwa munthu, ayenera kuyankha kuti “Wa alaikum” (ndi kwa inu nonse). 28. Akakumana Asilamu awiri, akamaliza salaam, …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 8
26. Ndi adab (makhalidwe a usilamu) kuti pamene munthu wina akuyenda, wina wakhala pansi, ndiye kuti oyendayo ayambe kupereka salaamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, pamene wina ali m’sitima yapamadzi ndipo wina akuyenda, ndiye kuti okwerayo ayenera kuyamba kupereka salamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, achichepere ayenera kupereka moni kwa akuluakulu, ndipo …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 7
21. Pamene mukudzithandiza, musapereke salaamu kwa munthu aliyense kapena kuyankha salamu ya munthu aliyense. Chimodzimodzinso, ngati munthu akudzithandiza, musamupatse salaamu. 22. Muyenera kupereka salaamu kwa akulu akulu anu modzichepetsa komaso ndi motsitsa mawu. 23. Ngati mwalonjeza kupereka salaamu ya munthu kwa wina, zimakhala Waajib kwa iwe kukwaniritsa lonjezo ndi kupereka …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 6
14. Amene wayambilira kupereka salaam amalandira Malipiro ochuluka. Abu Umaamah radhwiyallahu anhu wanena kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Amene amayambilira kuwalonjera anthu ena popereka salaamu amadziyandikitsa chifupi kwambiri mwa iwo kwa Allah (amakhala pafupi kwambiri ndi chifundo cha Allah). 15. Munthu akakupatsirani salaamu ya munthu, muyankhe ponena kuti “Alaikum …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 5
12. Pangani salaam polowa m’nyumba. Ngati m’nyumba mulibe aliyense, muyenera kupereka salaamu ponena kuti: السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللَّهِ الصَّالِحِينَ Mtendere ukhale pa ife ndi pa akapolo abwino a Allah. Olemekezeka Anas radhwiyallahu anhu adati: nthawi ina Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adandiuza kuti: “E iwe mwana wanga okondedwa,ukamalowa m’nyumba mwako, …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 4
9. Mawu a salaam amathera ndi “Wa barakaatuhu”. Munthu asawonjezere mau ena pambuyo pa “Wa barakaatuhu” Muhammad bin Amr bin Ataa rahimahu-Allah adanena kuti: Nthawi ina ndidali chikhalire ndi Abdullah bin Abbaas radhwiyallahu anhu pamene munthu wina ochokera ku Yemen adafika pamalopa ndipo adapereka salaam kuti: “Assalaamu alaikum wa rahmatullahi …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 3
6.Ziri Makruhu kupereka salaam kwa munghu yemwe watangwanika ndi ntchito ina ya Dini kapena akudya. 7. Musapereke salaam kwa omwe sali Mahram (Siwachibale). Ngati mkazi yemwe sali Mahram wapereka salaamu kwa mwamuna, koma kuti okalamba, ndipo palibe kuopa fitnah, akhonza kuyankhidwa. Komabe, ngati ndi mtsikana akupanga salaam, ndiye kuti munthu …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 2
3. Njira ya Sunnat yakaperekedwe ka salaam ndi kupereka moni kwa Asilamu onse, osati achibale ake, abwenzi ake ndi amene akuwadziwa okha. Olemekezeka Abdullah bin Amr radhwiyallahu anhu akusimba kuti munthu wina adamufunsa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam “Kodi ndi chikhalidwe chanji ndi mChisilamu chomwe chili choyamikirika komanso chabwino?” Adayankha Mtumiki …
Read More »Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 1
1. Ukakumana ndi Msilamu nzako, mupatse salaamu. Olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu akunena kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Msilamu ali ndi ma ufulu asanu ndi umodzi pa Msilamu nzake. Akakumana naye amlonjere (ndi salamu); ngati amuitana avomere kuitana kwake; akayetsemula amupangire duwa ponena kuti. ‘Yarhamukallah’ akadwala azikamuona akamwalira aziperekeza nawo …
Read More »
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu