Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 6

14. Amene wayambilira kupereka salaam amalandira Malipiro ochuluka.

Abu Umaamah radhwiyallahu anhu wanena kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Amene amayambilira kuwalonjera anthu ena popereka salaamu amadziyandikitsa chifupi kwambiri mwa iwo kwa Allah (amakhala pafupi kwambiri ndi chifundo cha Allah).

15. Munthu akakupatsirani salaamu ya munthu, muyankhe ponena kuti “Alaikum wa alaihimus salaam”. Komabe, ngati wina ayankha mongonena kuti “Wa alaikumus salaam” zidzakhala zokwanira.

16. Ndi waajib kuyankha salaamu yomwe yalembedwa mu kalata/SMS/imelo ndi zina zotero.

17. Sikoyenera kulemba salaamu mwachidule (monga slmz, salaams, etc.). Izi sizikugwirizana ndi kulemekezeka kwa salaamu. Ngati salaam inalembedwa mwachidule (monga,slmz,salaams ndi zina) sizidzakhala waajib kuyankha.

18. Ngati mwafika pa gulu limene akukambitsana kapena kukambirana za Dini, musapereke salaamu chifukwa zimenezi zidzasokoneza oyankhula nkhaniyo komanso amene ali pa zokambiranapo.

19. Ngati munthu watanganidwa ndi zokambirana kapena akugwira ntchito inayake ndi bwino osamupatsa salaam. Komabe, ngati wina akudziwa kuti sangadandaule ndiye kuti akhonza kupereka salaam.

20. Nkosaloredwa ( makruh-e-tahriimi) kuwerama popereka salaamu.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …