
Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akusimba kuti nthawi ina, nthawi ya Swalah ya Fajr, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati kwa Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu): “E, Bilaal! Pa ntchito zabwino zomwe umachita mchisilamu, ndi ntchito iti yomwe imakulimbikitsa kuti udzapindula nayo pa tsiku lachiweruzo,chifukwa usiku wapitawu ndamva kuyenda kwa mapazi ako ku Jannah (ku maloto).
Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha: “Zabwino zomwe ndimachita zomwe ndikuyembekeza kuti zidzandipindulira kwambiri, ndikuti nthawi iliyonse ndikapanga wudhu, kaya ndi masana kapena usiku, ndimaswali ndikamaliza kupanga wudhu (ndimaswali swalah ya Tahiyyatul Wudhu). (Muslim #2458)
Mu Hadith iyi, tikuona kuti chifukwa choswali Tahiyyatul wudhu, Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) adadalitsidwa ndi ulemelero okhala pamodzi ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ku Jannah kumaloto. Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akuyenda kutsogolo kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kutha kuoneka ngati momwe khaadim (wantchito) amayendera patsogolo pa mbuye wake kuti azimutumikira ndi kumuthandizira.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu