21. Pamene mukudzithandiza, musapereke salaamu kwa munthu aliyense kapena kuyankha salamu ya munthu aliyense. Chimodzimodzinso, ngati munthu akudzithandiza, musamupatse salaamu.
22. Muyenera kupereka salaamu kwa akulu akulu anu modzichepetsa komaso ndi motsitsa mawu.
23. Ngati mwalonjeza kupereka salaamu ya munthu kwa wina, zimakhala Waajib kwa iwe kukwaniritsa lonjezo ndi kupereka salaamu.
24. Sunnat ya salaam siili kwa akulu akulu okha. Munthu akakumana ndi ana, ayeneranso kuwalonjera ndi salaam. Olemekezeka Nabiy swallallahu alaihi wasallam akakumana ndi ana, ankawapatsa salaamu.
25. Mukakumana wina ndi nzake, muyambe kukambirana kwanu ndi salaam.
Olemekezeka Jaabir radhwiyallahu anhu akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Salaam iyambe kuperekedwa kukambirana kusanayambe.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu