Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 8

26. Ndi adab (makhalidwe a usilamu) kuti pamene munthu wina akuyenda, wina wakhala pansi, ndiye kuti oyendayo ayambe kupereka salaamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, pamene wina ali m’sitima yapamadzi ndipo wina akuyenda, ndiye kuti okwerayo ayenera kuyamba kupereka salamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, achichepere ayenera kupereka moni kwa akuluakulu, ndipo kagulu kakang’ono (ochepa m’chiŵerengero) kayenera kupereka moni ku gulu lalikulu (ochuluka).

Olemekezeka Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) wanena kuti Mtumiki (Sallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene wakwera pachombo ayambilire kupereka salam kwa amene akuyenda. Amene akuyenda apereke salaam kwa amene ali chikhalire.

Zindikirani: Ngakhale chikhalidwe cha Chisilamu ndikuti magulu awa omwe atchulidwa mu Hadith ayambilire kupereke salaam, komabe aliyense ayesetse kuyambilira popereka salaam, monga momwe zinaliri sunna ya Mtumiki (Sallallahu alaihi wasallam) kuyambilira kupereka salaam akakumana ndi munthu.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …