Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 9

27. Wina asapereke salaamu pomlonjera munthu amene si Msilamu. Ngati amene sali Msilamu apereka moni wa salaamu, ayankhe pongonena kuti “Wa alaik” (ndi pa inu), ndipo ngati ambiri omwe si Asilamu apereka salaam kwa munthu, ayenera kuyankha kuti “Wa alaikum” (ndi kwa inu nonse).

28. Akakumana Asilamu awiri, akamaliza salaam, achite Musaafahah (Kugwirana chanza).

Olemekezeka Abdullah Bun Masuud (radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Sallallahu alaihi wasallam) adati: “(Akakumana Asilamu awiri) kumaliza kwakulonjerana kwawo ndiko kuchita Musaafahah wina ndi mnzake.”

29. Popanga musaafaha, zili sunnah kupanga musaafaha ndi manja onse awiri.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …