Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 10

30. Popanga musaafah, ingogwirani manja a munthuyo, Palibe chifukwa chogwirana chanza ndikumavinitsa monga amachitira ma kuffaar. Chimodzimodzinso sizoyenera kupanga musaafahah uku ndikumapsopsona dzanja lake ndikumasisita pachifuwa chake popeza machitidwewa alibe maziko mu Dini.

31. Popanga musaafah, musagwire manja a munthu winayo momufinya mpaka kumupweteka.

32. Musafulumire kuchotsa manja anu mukapanga Musaafaha. M’malo mwake, muyenera kumusiira iyeyo kuti ayambilire kuchotsa dzanja lake.

Olemekwzeka Anas radhwiyallahu anhu akusimba kuti munthu akakumana ndi Mtumiki swallallah alaihi wasallam ndikugwirana chanza, Mtumiki swallallah alaihi wasallam sankachotsa dzanja lake pokhapokha munthuyo achotse. Komanso Mtumiki swallallahu alaihi wasallam sankatembenuka nkhope yake (kuchoka pamalo okumanirana) mpaka winayo atatembenuzira nkhope yake kwina (kuti adzipita kuchoka pamalopo).

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …