Ubwino wa Jumuah

Kukhululukidwa Kwa Machimo kudzera mukuswali Jumuah

Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Machimo omwe achitika pakati pa Jumu’ah ziwiri, ngati sali machimo akuluakulu, Allah amakhululuka.

Tsiku Lopatulika kwa Okhulupirira

Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) adanena kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Tsiku ili (tsiku la Jumu’ah) ndi tsiku la Eid limene Allah adawapatsa asilamu, ndipo aliyense amene akubwera kudzaswali akuyenera kusamba, ndipo amene angakhale ndi mafuta onunkhiritsa monga pelefyumu apake, ndipo ndikukulimbikitsani kuti mugwiritse ntchito miswaak”

Tsiku Lomwe Lili ndi Mphindi Zopatulika Zomwe maduwa Amayankhidwa

Anas bun Maalik radhwiyallahuanhu akusimba kuti: Tsiku la Jumaa linaperekedwa kwa Mtumiki swallallahu alaihiwasallam. Jibriil alaihis salaam adadza kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam dzanja lake likuwala ngati galasi lodziyang’anira, ndipo pakati pa galasilo panali dontho lakuda. Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adamufunsa Jibril alaihis salaam kuti: “Ndichiyani ichi Jibriil” Jibriil alaihis salaam anayankha nati: “Galasi lodziyang’anira lomwe likuimira tsiku la Jumu’ah lomwe lidaperekedwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu kuti chikhale Eid kwa inu ndi Ummah wanu. Muli ubwino wambiri m’menemo. Chifukwa chakuti mwalandira tsiku loyamba (kuchokera Lachisanu, Loweruka ndi Lamlungu), mudzakhala oyamba (kulowa mu Jannah ndi otsatira anu), ndipo Ayuda ndi Akristu (omwe adalowa Chisilamu mu nthawi ya Ambiyaa alaihimus salaam adzabwera pambuyo panu. Pa tsiku la Jumu’ah, pali nthawi yapadera yolandiridwa maduwa. Aliyense amene apempha dua kwa Mbuye wake mu nthawi imeneyo pa zabwino zilizonse zomwe zamuyenera, Allah adzamupatsa, ndipo aliyense amene akufuna chitetezo ku zoipa, Allah adzachotsa choipacho komanso chipsinjo chachikulu kwa iye. Tsiku Lomaliza lidzatchedwa kuti “Tsiku Lowonjezera” (kwa anthu a ku Janna omwe adzapatsidwe mwayi omuona a Allah ndi kuchuluka kwa madalitso pa tsikuli).”

Zindikirani: Dontho lakuda likutanthauza tsiku laJumu’ah lomwe lidzakhale tsiku lomaliza padziko lapansi. M’ Hadith ya Musnad Abi Ya’laa, zanenedwa kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: “Masiku adaonetsedwa, ndipo mwa iwo Lachisanu lidasonyezedwa kwa ine, Lidafanana ndi kalilole onyezimira, lomwe mkati mwake munali dontho lakuda,ndinamufunsa Jibriil kuti dontho lakudalo limatanthauzanji? Iye anayankha nati.: “Ndi Jumuah yomaliza (yomwe Qiyamah idzachitike Qiyaamah).

Tsiku Lachikhululuko

Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Allah” Sasiya aliyense mwa Asilamu pa tsiku la Jumu’ah popanda kuwakhululukira (omwe akusamala malamulo a Allah).

Kumwalira Tsiku La Jumu’ah

Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe Msilamu amene amamwalira masana kapena usiku wa tsiku la Jumu’ah koma kuti Allah amamupulumutsa ku mavuto am’manda.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …