1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku.
Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati, munthu amene amawerenga Surah Haa-meem Ad-Dukhaan usiku wa Jumu’ah ( Lachinayi usiku), machimo ake adzakhululukidwa.”
2. Sambani (ghusl) Lachisanu. Munthu amene amasamba Lachisanu, machimo ake ang’onoang’ono amakhululukidwa.
Olemekezeka Abu Bakr Siddeeg (radhwiyallahj anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahh alaihi wasalllam) adati: “Amene angasambe tsiku la Jumuah, adzakhululukidwa machimo ake ang’onoang’ono.”
3. Chotsani tsitsi losafunika, ndipo wengani zikhadabo zanu tsiku la Jumuah.
4. Tsukani mkamwa mwanu ndi miswaak ndikudzipaka pelefyumu.
Olemekezeka Abu Sa’eed Khudri (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaiji wasllam) adati, “Munthu aliyense baaligh (otha msinkhu) tsiku la Jumuah ayenera kusamba, gwiritsani ntchito miswaak ndikudzola pelefyumu.
5. Valani zovala zanu zabwino kwambiri tsiku la Jumu’ah.
Olemekezeka Abdullah bin Salaam (radhwiyallahu anhu) akunena kuti anamumva Rasulullah (swallallahu alaihi wasalllam) akuyankhula ali pa mimbar, akupereka khutbah tsiku la Jumu’ah, “Bwanji osagula zovala ndikuzisunga padera kuti muzivala tsiku la Jumu’ah, kupatula zovala zanu zatsiku ndi tsiku?
6. Ndikwabwino kuvala zovala zoyera.
Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Valani zovala zoyera; Ndithu, ndi chovala chabwino kwambiri;
7. Zanenedwa kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) nthawi zina ankawerenga Surat Sajdah mu rakaat yoyamba ndi Surah Dahr mu rakaat yachiwiri ya Swala ya Fajr tsiku la Jumuah. Choncho, wina Nthawi zina ayenera kuwerenga ma Surah awa pa Swala ya Fajr tsiku la Jumu’ah.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu