Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 2

8. Pitani mwamsanga ku mzikiti kukaswali Jumu’ah, momwe mungapitire mwamsanga ndi momweso mungalandilire mphotho yochuluka.

Olemekezeka Abu Hurairah radhwiya-Allahu ‘anhu akusimba kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati, “Amene amasamba ngati momwe amasambira akakhala ndi janaabah (i.e. amasamba mosamaritsa monga momwe amachitira akakhala ndi janaabah), ndikupita ku Jumu’ah Salaah moyambilira, amalandira mphotho yofanana ndi amene wapereka ngamila chifukwa cha Allah, ndipo aliyense amene wapita ku Jumu’ah Salaah ndikukhala wachiwiri, amalandira mphotho yofanana ndi amene wapereka ng’ombe chifukwa cha Allah , ndipo aliyense amene apita ku Jumu’ah Salaah nakhala wachitatu, amalandira mphotho yofanana ndi amene wapereka nkhosa yomwe ili ndi nyanga chifukwa cha Allah, ndipo aliyense amene wapita ku Jumu’ah Salaah ndikukhala wachinayi amalandira mphotho yofanana ndi amene wapereka nkhuku mu njira Allah, ndipo aliyense amene wapita ku Jumu’ah Salaah ndi kukhala wachisanu, amalandira mphotho yofanana ndi yemwe wapereka mnjira ya Allah.

Check Also

Ubwino wa Jumuah

Kukhululukidwa Kwa Machimo kudzera mukuswali Jumuah Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi …