Kutsatira kwa Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Malangizo a Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam

Ma’roor bin Suwaid (rahimahullah) akufotokoza izi:

Nthawi ina tinadutsa kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) ku Rabzah ndipo tinaona kuti anali atavala zovala ziwiri. Chimodzi chinali chakale, pomwe china chinali chatsopano, ndipo kapolo wake nayenso anali atavala zovala ziwiri, zomwe chimodzi chinali chatsopano ndipo china chinali chakale.

Kenako tidati kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu), “Oh Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)! Ngati mungavale zovala zonse ziwiri zatsopano (pomupatsa kapolo wanu nsalu yakale yomwe mwavala ndikutenga nsalu yatsopano), zonse zikhala zatsopano ndipo zigwirizana.”
Poyankha, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anafotokoza chifukwa chomwe ankachitira zimenezi kwa kapolo wake pomupanga kukhala ofanana ndi iye mwini akunena kuti:

Nthawi ina, mkangano unabuka pakati pa ine ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu). Nthawi yonse yomwe timkanganayi, ndinamunyoza chifukwa cha amayi ake. Ndinamuuza kuti, “Ndiwe mwana wa mkazi wakuda.” Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) anakhumudwa ndi izi ndipo anakadandaula kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) za zomwe ndinamuuza.

Pambuyo pake nditakumana ndi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), anandiuza kuti, “O Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu)! Ndiwe munthu amene ukadali ndi makhalidwe a nthawi ya u Jaahiliyyah (umbuli).” Ndinadabwa ndipo ndinati kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), “Kodi ndi zoona kuti ndikadali ndi makhalidwe a mu umbuli mwa ine”? Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Eya, udakali ndi makhalidwe a u Jaahilyyah mwa iwe (kuti umadziona kuti ndiwe opambana kuposa Bilaal).”

Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) atamva izi kuchokera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), anakhudzika kwambiri kotero kuti anagona pansi nati, “Sindidzuka mpaka Bilaal ataika phanzi lake pa tsaya langa ngati dipo la mawu omwe ndinayankhula.” Bilaal (radhwiyallahu anhu) ataika phanzi lake pa tsaya la Abu Zar (radhwiyallahu anhu) ndipomwe iye anakhutira kenako anadzuka.
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kenako anamulangiza Abu Zar (radhwiyallahu anhu) mwachikondi momwe ayenera kuchitira ndi akapolo. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Ndi abale anu ndi akapolo anu omwe Allah Ta‘aala wawaika m’manja mwanu. kotero, muyenera kuwadyetsa kuchokera ku chakudya chomwe mumadya, kuwaveka kuchokera ku zovala zomwe mumavala, ndipo musawalemetse ndi zomwe sangakwanitse. Ngati muwalemetsa ndi ntchito yovuta, onetsetsani kuti mwawathandizira (kuti akwaniritse).”

Chifukwa cha uphungu uwu wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) Hazrat Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) adakumbukira kuti m’moyo wake onse, ankachita zinthu ndi akapolo ake mwanjira imeneyi.

(Saheeh Muslim #1661, Saheeh Bukhaari #30, Fat-hul Baari 1/106, Ibn Sa’d 4/179)

Check Also

Kulowa Chisilamu kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Khalidwe lake Asanalowe Chisilamu: Asanalowe Chisilamu, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anali chigawenga. Anali olimba mtima …