Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 3

9. Ngati n’kotheka, yendani wapansi popita ku musjid kukaswali swalaah ya Jumu’ah. Phanzi lirilonse lomwe mungaponye, mudzalandira mphotho ya kusala kudya kwa chaka chimodzi ndi Tahajjud.

Olemekezeka Aws bin Aws Thaqafi radhwiya-Allah anhu akuti, “Ndidamva Rasulullah swallallahu alaihi wasallam akunena kuti, ‘Munthu amene amachita ghusl tsiku la Jumu’ah ndipo amapita ku musjid nthawi yabwino poyenda wapasi, ndipo sapita pa chokwera, ndipo amakhala pafupi ndi imaam ndikumvetsera khutbah mosamala, ndipo sachita chilichonse chopanda pake, Iye adzalandira mphotho ya kusala kudya kwa chaka chimodzi ndikuswali Tahajjud pa phanzi lirilonse lomwe amatenga angayende kupita ku musjid.””

10. Mvetserani khutbah mwachidwi, ngakhale simukuimva. Musalankhule kapena kulangiza ena kuti akhale chete pamene khutbah ikuchitika.

Olemekezeka Ibnu Abbaas radhwiyallahu anhu akunena kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: “Fanizo la yemwe amayankhula tsiku laJumu’ah pamene imaam akupanga khutbah zili ngati bulu amene amanyamura mabuku ambiri kumbuyo kwake (monga momwe bulu amene amanyamula mabuku ambiri a Deeni kumbuyo kwake sapindura ndi mabuku a Deeni, momwemonso amene amalankhula khutbah ikuchitika sadzalandira phindu lililonse). Ndipo amene amauza wina kuti akhale chete (pamene khutbah ikuperekedwa), palibe Jumu’ah kwa iye. (ngakhale akulangiza wina kuti akhale chete panthawi ya khutbah, iye mwini wachita tchimo chifukwa cholankhula pamene khutbah ikuchitika).

Check Also

Ubwino wa Jumuah

Kukhululukidwa Kwa Machimo kudzera mukuswali Jumuah Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi …