
Abu Zar Ghifaari (Radhwiyallahu ‘anhu) anali Sahaabi yemwe ankafanana ndi Nabiy Isa (‘alaihis salaam) m’maonekedwe ake komanso kukongola kwake.
Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Aliyense amene akufuna kumuona Isa bin Maryam (‘alaihis salaam) Taqwa yake, chilungamo chake, ndi kudzipereka kwake (pa ibaadah), ayenera kumuyang’ana Abu Zar” (Majmauz Zawaaid #15817)
Chimodzimodzinso, mu Hadith ina, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Aliyense amene akufuna kuona munthu ofanana ndi Isa (‘alaihis salaam) m!maonekedwe ake ndi makhalidwe ake, ayenera kumuyang’ana Abu Zar.” (Majmanz Zawaaid #15820)
Ena mwa makhalidwe abwino a olemekezeka Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) omwe adawonekera kwambiri ndi khalidwe lake losalilabadira dziko lapansi. Atalowa Chisilamu, adakhala moyo wake ofanana ndi Ambiya (alaihimus salaam) posonyeza kusakonda dziko lapansi. Cholinga chake chonse ndi kudzipereka kwake zidaperekedwa ku umoyo waku Aakhirah kuti akapeze chisangalalo kwa Allah Ta’ala
Zonsezi anazipeza chifukwa cha madalitso a kukhala chifupi ndi Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), asanalowe Chisilamu, chikondi chake pa chuma cha dziko lapansi chinali chachikulu kwambiri kotero kuti ankatha kuchitira za uchifwamba anthu kuti akapeze chuma.
Zanenedwa kuti chikondi cha chuma chinachoka mumtima mwake atamva machenjezo amphamvu ochokera kwa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) kwa iwo omwe sakwaniritsa ufulu wa chuma chomwe Allah Ta’ala wawapatsa. Chimodzimodzinso Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) ataona moyo odziletsa omwe Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) ankatsogolera, ankakonda moyo odzitalikitsa ndi zisangalalo za dziko lapansi.
Nthawi ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adali atakhala pamthunzi wa Kabah Shariif. Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) atalowa mu nzikiti adamumva Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) akunena kuti, “Ndikulumbira mwa Mbuye wa Kabah, iwo ndi otayika kwambiri (ndipo adzalangidwa ndi moto wa Jahannum)!” Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anabwereza chenjezoli kawiri konse.
Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) adali ndi nkhawa kwambiri ndipo anati mumtima mwake, “Kodi pali vesi lililonse lomwe lavumbulutsidwa lokhudza ine?” (chifukwa chiyani Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam) wayankhula izi)?” Choncho anapita kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anapitiriza kunena kuti, “Ndikumbira mwa Rabb wa Kabah, iwo ndi otayika kwambiri (ndipo aweruzidwa kukalowa ku moto wa Jahannum)”
Abu Zar (radhwiyallahu anhu) adafunsa kuti, “Oh Rasul wa Allah, amayi anga ndi abambo anga aperekedwe nsembe chifukwa cha inu. Kodi chenjezo ili ndi la ndani?” Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ndi la iwo amene amasonkhanitsa chuma, iwo ndi otayika (ndipo adzaweruzidwa kuti adzakalowe kumoto wa Jahannam), kupatula iwo amene amapereka mwachifundo kudzanja lawo lamanja, kumanzere kwawo, kutsogolo ndi kumbuyo (kukwaniritsa ufulu wa chuma).” (Sahiih Bukhaari #6638, Musnad Ahmad #21491, Fathul Baari 11/298)
Mukunena kwina, amene akugwiritsa bwino ntchito chuma chawo popereka kwa osauka zakaat ndi kukwaniritsa maudindo awo ena okhudzana ndi chuma (monga kugwiritsa ntchito ndalama pa mabanja awo, kulipira ngongole zawo ndi zina zotero), ndiye kuti kwa anthu otere, chumacho sichidzakhala njira yoti akalowe ku moto ndi kulangidwa.
Chimodzimodzinso, nthawi ina, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anali ndi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) ku Madinah Munawwarah pafupi ndi Phiri la Uhud. Inali nthawi ya maghrib, pamene dzuwa linali pafupi kulowa. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adamulankhula nati, “E Abu Zar! Phiri la Uhud lomwe lili patsogolo pathu Allah akadati alisinthe phiri ili kukhala golide kwa ine, sindikanakonda kusunga golideyo kwa masiku atatu, mpaka nditapereka yense kwa osauka, kupatura kusunga dinaar pambali kuti ndilipire ngongole yomwe ndili nayo.” (Saheeh Bukhaari #6444)
Kotero zidaimira Abu Zar Ghifaari (radhwiyallahu ‘anhu) kuyang’ana moyo wa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) olisala dziko lapansi, komanso kumva machenjezo owopsya kwa omwe ali ndi chuma koma samachigwiritsa ntchito moyenera ndi ufulu omwe ali nawo kwa ena pa chuma, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) adakulitsa mkwiyo ndi chidani pa dziko lapansi, kotero kuti sanasunge chuma ndipo sankakonda kuona anthu akusunga chuma chochulukirapo.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu