Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 4

11. Werengani durood mochuluka.

Olemekezeka Aws bin Aws radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Masiku abwino kwambiri ndi tsiku la Jumuah.

12. Yesetsani kuwerenga duruud chikwi chimodzi (ka 1000) tsiku la Jumuah.

Olemekezeka Anas radhwiyallahu anhu akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Amene amawerenga duruud pa ine chikwi chimodzi tsiku la Jumuah sadzachoka padziko lapansi mpaka ataonetsedwa nyumba yake ku Paradiso.”

13. Ndi sunnah kuwerenga Surah A’ala mu rakaat yoyamba ya Swala ya Jumu’ah ndi Surah Ghaashiyah mu rakaat yachiwiri. Komanso zili sunnah kuwerenga Surah Jumu’ah mu rakaat yoyamba ya Swalaah ya Jumu’ah ndi Surah Munaafiquun mu rakaat yachiwiri.

14. Werengani Surah Kahf musanaswali Swalah kapena mukatha kuswali. Malinga ndi hadith ina, kuwerenga kwa Surah Kahf kumapangitsa kuti munthu akhululukidwe machimo ake ang’onoang’ono a sabata yapitayi.

Olemekezeka Ibnu Umar radhwiyallahu anhuma akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: Amene angawerenge Surah Kahf tsiku la Jumu’ah, kuwala (noor) kumatuluka pansi pa mapazi ake ndikufalikira kumwamba. Nuur iyi idzamuwalira iye pa tsiku la Qiyaamah, ndipo Adzakhululukidwa machimo ake onse (Ang’onoang’ono) amene adachita pakati pa Jumuah ziwiri.”

15. Ndikoloredwa kupanga dua chamu m’mtima pakati pa ma khutba awiri. Simukuyenera kukweza manja anu kapena kugwedeza milomo yanu pamene mukupanga dua panthawiyi.

Check Also

Ubwino wa Jumuah

Kukhululukidwa Kwa Machimo kudzera mukuswali Jumuah Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi …