Olemekezeka Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) asamukira ku Shaam ndi Rabadhah

Zidatengera Abu Zarr Ghifaari (radhiyallahu ‘anhu) kuphunzira moyo wa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) osasamala za moyo wadziko lapansi komanso kudziletsa ndi kumvera machenjezo amphamvu kwa omwe ali ndi chuma koma osagwiritsa ntchito moyenera, Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) adayamba kudana ndi dziko lapansi kotero kuti sanasunge chuma ndipo sankakonda kuona anthu akusunga chuma chochuluka.

Kudana kwambiri ndi chuma kumeneku kunamupangitsa Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) kuti azilangiza anthu a ku Madinah Munawwarah kuti asamasunge chuma chodutsa pa mlingo omwe akufunika kugwirotsa ntchito.

Anthu a ku Madinah Munawwarah anayamba kuvutika ndi Abu Zarr (radhwiyallahu anhu) akuwachenjeza mosalekeza kuti asamasunge chuma china chilichonse, Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamupempha kuti asamukire ku Shaam. Kudzera mwa iye kukhala ndi anthu ku Shaam, zinali zovuta kuti aone anthu okhala ndi chuma chochuluka ndipo anayamba kuwachenjeza ndi kuwadzudzula chifukwa chosunga chuma chambiri, kufikira kuti anthu anayamba kuganiza kuti n’kovuta kukhala naye.

Pa chifukwa chomenechi, Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamuitananso ku Madinah Munawwarah, koma poona kuti zinali zovuta kuti akhale ndi anthu kuno chifukwa cha chifukwa chomwecho, Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) pamapeto pake adamupempha kuti asamukire ku Rabadhah malo omwe ali patali ndi Madinah Munawwarah.

Chilichonse chomwe chinamuchitikira Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) pa moyo wake onse, monga kuyenda kuchokera pamalo ena kupita kwina, kwenikweni chinali chimene Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) analosera.

Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti:

Nthawi ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anabwera kwa ine ndiri mtulo mu Mzikiti wa Madinah Munawwarah. Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anandikhudza ndi phazi lake lodalitsika kuti andidzutse ndipo anandiuza kuti, “Kodi sindikuona ukugona mu musjid?” Ndinayankha kuti, “Eh Nabi wa Allah! Ndinagona tulo tofa nato!”

Kenako Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Udzachita chiyani ukatulutsidwa mmenemo (monga kuchotsedwa mumzinda odala wa Madinah Munawwarah)?” Ndinayankha kuti, “Ndidzapita dziko lopatulika, lodalitsika la Shaam.”

Kenako Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Udzachita chiyani ukadzatulutsidwa ku Shaam?” Ndinayankha kuti, “Ndidzabwerera kumeneko (ku mzinda odalitsika wa Madinah Munawwarah).”

Kenako Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Udzachita chiyani ukadztulutsidwa m’menemo ( Madinah Munawwarah kachiwiri)?” Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Ndidzachite chiyani, Ee Nabi wa Allah? Ndikanthe ndi lupanga langa (ndi kumenyana ndi amene akufuna kunditulutsa)?”

Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anayankha kuti, “Kodi ndisakuonetse chomwe chili chabwino kwa iwe kuposa chimenecho komanso cholondola? uyenera kumvetsera ndi kumvera, ndipo udzalole kuti akutengere kulikonse komwe akufuna kukutengera.” (Musnad Ahmad # 21382)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …