Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) Alemekeza kwambiri Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu)

Munthu wina ochokera ku fuko la Banu Sulaym adayankhula izi:

“Nthawi ina ndinakhala pa gulu lomwe Abu Zarr anali pomwepo. Maganizo anga anali oti mwina Abu Zarr wamukwiyira Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) chifukwa choti Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adamupempha kuti asamuke ku Madinah Munawwarah ndikukakhala ku Rabadha.

Pagulupo wina adapereka ndemanga yomutsutsa Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu). Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) atamva ndemanga yoipa ya munthuyo yokhudza Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu), nthawi yomweyo anayankha kuti:

“Musayankhule chilichonse chokhudza Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) kupatula zabwino, chifukwa ine ndi mboni kuti inalipo nthawi yomwe ndinaona chinthu chapadera chikuchitika ndi Uthmaan (radhwiyallahu anhu) chomwe sindimaiwala.

“Nthawi ina, ndinapempha chilolezo chokhala ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) ndekha kuti ndipindule naye ndikutsatira malangizo omwe angandipatse.

“Nditakhala ndekha ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kwa kanthawi, Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) anabwera pamaso pa Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam), kutsatizana ndi Umar (radhwiyallahu anhu), kenako Uthmaan (radhwiyallahu anhu). Onse anabwera kwa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam), mmodzi pambuyo pa wina, mukudutsa kwa nthawi yochepa.

“Tili chikhalire chomwecho, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), anatenga miyala ina m’dzanja lake lodalitsika, ndipo miyala ina inayamba kuwerenga tasbiih m’dzanja lake. Tasbiih ya miyala inkachita kumveka ndipo inkamveka ngati kulira kwa njuchi. Kenako anapereka miyalayo kwa Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu), ndipo iyo inapitiriza kupanga tasbiih m’dzanja lake. Ataiyika pansi, inakhala chete.

“Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) kenako anaipereka kwa Umar (radhwiyallahu ‘anhu), ndipo inayambiranso kuwerwnga tasbiih m’dzanja lake. Pambuyo pake, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anaitenga kwa Umar (radhwiyallahu anhu) naiyika pansi, ndipo inakhala chete.

“Pambuyo pake, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaipereka kwa Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu), ndipo pameneponso inayamba kuwerenga tasbiih m’manja mwake. Kenako adaitenga kwa iye ndikuyiika pansi, ndipo idakhala chete.” (Siyar A’laamin Nubala 2/453)

Check Also

Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Apereka Uphungu kwa Mtsogoleri wa Asilikali Kuti Atsatire Chilungamo

Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akunena kuti: Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu) pamene adali bwanamkubwa wa …