
Tsiku lina munthu ochokera ku fuko la Banu Sulaim anabwera kwa Abu Zarr (radhwiyallahu anhu) ndipo anamuuza kuti: “Ndikufuna kukhala nanu kuti ndipindule ndi maphunziro anu a malamulo a Allah Ta’ala ndi ma sunnah a Nabi swallallahu alaihi wasallam Inenso ndidzathandiza wantchito wanu kusamalira ngamila.”
Abu Zarr radhwiyallahu anhu anayankha kuti: “Sindingathe kukhala ndi munthu amene sangandimvere, koma ngati nthawi zonse ungachite zomwe ndikukuuza, ndiye kuti utha kukhala nane, apo ayi siungathe kukhala nane.”
Munthuyo anafunsa kuti: “Ndi zinthu ziti zomwe mungafune kuti ndikumvereni?”
Abu Zarr radhwiyallahu anhu anayankha kuti: “Ndikakupempha kuti ugwiritse ntchito ndalama kuchokera ku katundu wanga, uyenera kugwiritsa ntchito mosamaritsa kwambiri.”
Munthuyo anafotokoza kuti, “Ndinavomereza mawu a Olemekezeka Abu Zarr ndipo ndinayamba kukhala naye.
Tsiku lina, munthu wina anauza Abu Zarr (radhwiyallahu ‘anhu) kuti panali anthu osauka omwe ankagona m’misasa pafupi ndi kasupe pafupi ndipo akusowa chakudya. Choncho iye (Abu Zarr) anandiuza kuti ndikatenge ngamila. Ndinapita ndipo ndinaganiza zosankha yabwino kwambiri, monga momwe ndinalonjezera. Inali nyama yachifundo komanso yomvera yomwe inali yabwino kukwera, choncho ndinaganiza zoisiya ndikusankha yapambuyo pake mu ubwino. Kupatula izo, inali yoti ingophedwa ndi kudyedwa ndipo pachifukwa ichi inali yabwino ngati inayo. Ina inali yabwino kwambiri kukwera ndipo inali yothandiza kwambiri kwa Abu Zarr radhwiyallahu anhu ndi banja lake, pomwe osauka akaganiza kuti iyi kuti ndi yokoma ngati inayo. Choncho, ndinatsogolera ngamila inayo ndikuipititsa kwa Abu Zarr radhwiyallahu anhu
Anandikalipira nati: Waswa lonjezo lako. Podziwa bwino zomwe amatanthauza, ndinabwerera ndikukatenga ngamila yabwino kwambiri m’malo mwake.
Iye (Abu Zarr) kenako anafunsa anthu omwe anali pafupi naye kuti, ‘Ndikufuna anthu awiri kuti agwire ntchito ya Allah Ta’ala. Anthu awiri anabwera patsogolo. Anawapempha kuti apite akaphe ngamilayo ndikuigawa nyama mofanana ku mabanja omwe anali m’misasa pafupi ndi madzi, kuphatikizapo banja lake, ndipo anati, ‘Banja langa lirandiranso mofanana ndi anthu ena onse omwe anali m’gawoli.’ Anthu awiriwa anatsatira malangizo ake.
Atagawa nyama ija, anandiitana nati kwa ine: ‘Kodi unanyalanyaza malangizo anga mwadala nditakuuza kuti ugwiritse ntchito chuma changa chonse, kapena unaiwala malangizo anga. Ngati zili choncho, ndikukhululukira chifukwa cha kulakwitsa kwako?’
Ndinayankha kuti: ‘Sindinaiwale malangizo anu, koma ndimaganiza kuti zingakhale bwino kusiya ngamila yabwino kwambiri kuti muzikwere, pomwe inayo inali yabwino kudya.’
Abu Zarr radhwiyallahu anhu anafunsa kuti: ‘Kodi unaisiya ndi cholinga izitukira ine basi?’ Ndinayankha kuti, “Inde.”
Abu Zarr radhwiyallahu anhu adati: Ndidzasiyidwa ndekha mumdima wa manda. Kumbukira, pali abwezi atatu mu chuma chako-: kenako anandilangiza kuti: ‘Bwera; ndikuuze za nthawi ya zosowa zanga. Limenelo ndi tsiku limene,
Oyamba, tsogolo lako, lomwe silimayembekezera kutenga gawo lake. Lidzatenga zonse zomwe liyenera kutenga, mosasamala kanthu kuti chuma ndi chabwino kapena choipa. Lidzatenga zonse zomwe liyenera kutenga.
Wachiwiri, alowa m’malo mwako akuyembekezera imfa yako mwachidwi, kuti adzatenge gawo lawo.
Wachitatu ndiweyo. Ngati ungathe, usakhale munthu osathandizidwa kudzera mwa atatuwa. Tenga gawo lako lonse, mene ungathere.
Allah Ta’ala akuti:
لَنْ تَنَالُوا الْبِرَّ حَتَّى تُنْفِقُوا مِمَّا تُحِبُّونَ
“Simudzafika pa chilungamo/kudzipereka mpaka mutagwiritsa ntchito zomwe mumakuzikonda.” (Surat Aale I’mraan – Aayah 92)
Choncho, ndikuganiza kuti ndi chanzeru kuti ndizitsogoza zabwino pa zimene ndimazikonda (ku Aakhirat), kuti zisungidwe kumeneko.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu