Fudhail bun Iyaaz (Rahimahullah) aDali Muhaddith olemekezeka komanso oyera mtima wa m’nthawi yake.
Allah Talaa adamdalitsa ndi ulemelero wapamwamba kwambiri mu Hadith kotero kuti ambiri mwa ma Muhadith otsogola, monga Abdullah bin Mubaarak, Sufyaan bun Uyainah ndi Imaam Shaafi’e (Rahimahullah) adafotokoza Hadith kuchokera kwa iye.
Zanenedwa kuti Fudhail (Rahimahullah) asanadalitsidwe ndi udindo wapamwamba mchipembedzo, ankadziwika kuti anali wachifwamba odziwika bwino wa m’misewu. Komabe Allah Talaa adamdalitsa ndi tawfiiq (kuthekera) kuti alape machimo ake ndi kukonza moyo wake.
Nkhani yonse yokhudza kulapa Kwake
Nthaŵi ina, gulu lina la kalavani linkayenda mumsewu umene Fudhail ankabera anthu. Mwa anthu omwe adali paulendowo panali Qaari yemwe ankawerenga Quraan Majiid mwanthetemya kwambiri.
Gululi likudutsa pafupi ndi Fudhail, Qaariy ankawerenga ndime iyi ya Quraan:
Kodi siinafike nthawi yoti mitima ya Asilamu ikhale yamantha pokumbukira Allah…?
Atamva aya iyi, mtima wa Fudhail udakhudzidwa kwambiri moti nthawi yomweyo adatembenukira kwa Allah Talaa kulapa ndikusiya moyo wamachimo.
Pambuyo pake, Fudhail (Rahimahullah) adalimbikira kuchita Ibadah ndi kupeza maphunziro a dini, mpaka idafika nthawi yomwe ngakhale Haarun Rasheed (Rahimahullah) mfumu ya nthawiyo, adayamba kumamuyendera kuti apindule ndi malangizo ake.
Mfumu, Haaroon Rasheed (rahimahullah) Kupindula Ndi Malangizo a Fudhail bin Iyaaz (rahimahullah)
Zanenedwa kuti nthawi ina Haarun Rashiid (rahimahullah) adachita Haji, adauza Fadhl bun Rabee kuti: “Ndikumva kufooka mu mtima mwanga. Choncho nditengereni kwa bwenzi loopa Allah Talaa kuti ndikamve malangizo kwa iye ndi kupindula naye.”
Fadhl adamulangiza kuti apite akakumane ndi Sufyaan bin Uyainah (rahimahullah) atafika kunyumba kwake pakhomo Sufyaan anamulandira ndi ulemu waukulu.
Haaruun Rashiid anamuuza. “Cholinga cha zomwe ndabwelera ndikudzapempha upangiri kwa inu.” Sufyaan kenako anamupatsa upangiri wamba.
Pomaliza pake, Haaruun Rashiid (rahimahullah) atafuna kuchoka, anafunsa Suyaan (rahimahullah). “Kodi muli ndi ngongole zilizonse zomwe ndingakuthandizeni kuzithetsa?” Sufyaan anayankha movomereza, ndipo Haaruun Rashiid (rahimahullah) anamulamula Fadhl kuti athetse ngongole zake.
Atachoka Sufyan Haaruun Rashiid anatembenukira kwa Fadhl nati, “Palibe ndapindula kwa Sufyaan (rahimahullah) momwe ndimafunira.” (Mwina Haaruun Rashiid (rahimahullah) sadakhutitsidwe chifukwa ankaona kuti Sufyaan (rahimahullah) amamupatsa ulemu kwambiri ndi kumulemekeza ndipo sanamuonetse kufooka kwake kulikonse.) Choncho Fadhl adanena kuti apite kwa Imaam Abdur Razzaaq (rahimahullah).
Imaam Abdur Razzaaq (rahimahullah) nayenso adamulandira Haarun Rashiid (rahimahullah) mwaulemu waukulu ndipo adamupatsa upangiri pa zomwe adapempha.
Asananyamuke, Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamufunsa: “Kodi uli ndi mangawa omwe ndingakuthandizireni?” Imaam Abdur Razzaag atayankha kuti ali ndi ngongole, Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamuuza Fadhl kuti athetse ngongolezo.
Apanso atachoka, Haaruun Rasheliid (rahimahullah) adati kwa Fadhl: “Sindinapindule ndi Imaam Abdur Razzaq (rahimahullah) monga momwe ndimafunira. Ndipezere munthu oyenera yemwe ndingathe kumupitira.” Fadhl adamuuza kuti apite akakumane ndi Fudhail bin Iyaaz (rahimahullah).
Atakumana ndi Fudhail Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamupempha kuti amupatse malangizo.
Fudhail adamuuza kuti, “Umar bin Abdil Aziiz atasankhidwa kukhala Khalifah, anaitana Saalim bin Abdillah, Muhammad bin Ka’b ndi Rajaa bin Haywah nati kwa iwo. ‘Ndayesedwa ndi mayesero awa a ulamuliro, choncho chonde ndilangizeni.'”
Fudhail adati, “Umar bin Abdil Aziiz anali ndi nkhawa kwambiri ndi Khilaafah kotero kuti adaitenga ngati ndi mayeso, pomwe inu mumaitenga ngati ndi mdalitso (ndipo mulibe nkhawa ngati iye).”
Fudhail (rahimahullah) anamuchenjeza kuti ngati sadzayang’anira zinthu za Khilaafah motsatira malamulo a shari’ah, ndiye kuti adzalangidwa ndi chilango cha Jahannum. Chenjezoli linamukhudza kwambiri Haaruun Rashiid (rahimahullah) kotero kuti anayamba kulira kwambiri.
Haaruun Rashiid akufuna zoti adzinyamuka adamufunsa Fudhail “Kodi muli ndi ngongole zilizonse zomwe mungafune kuti ndikuthandizeni kubweza? Fudhail (rahimahullah) anayankha, “Inde! Ndili ndi ngongole zomwe ndi ufulu omwe ndili nawo kwa Mbuye wanga. Ngati mukufuna kundithandiza mutha kutero.”
Kenako Haaruun Rashiid adapereka ndalama kwa Fudhail nati, “Nazi ma dinar chikwi. Landirani kuchokera kwa ine ngati mphatso ndipo mugwiritse ntchito kwa omwe amadalira inu.”
Fudhail (rahimahullah) anayankha “Subhaanallah! Ndakuwonetsani njira yopezera chipulumutso, ndipo umu ndi momwe mukundibwezera? Mukupereka chuma ichi kwa munthu amene alibe chosowa. Muyenera kuchipereka kwa amene akuchisowa.”
Haarun Rashid (rahimahullah) ndi Fadhl pambuyo pake adachoka ku nyumba ya Fudhail (rahimahullah) Haarun Rashid (rahimahullah) adati kwa Fadhl: “Oh Fadhl! ukafuna kunditengera kwamunthu aliyense uzinditengera kwameneyu,Ndithu, Uyu ndi Mtsogoleri wa Asilamu onse!”
Haarun Rashid (rahimahullah) adachita chidwi kwambiri ndi Fudhail (rahimahullah) chifukwa cha makhalidwe abwino omwe adali nawo – kuopa kudzayankha mlandu wake pa Tsiku Lomaliza, kuopa kwake kwakukulu, kusakondweretsedwa kwake ndi zapadziko lapansi, kudzipereka kwake mu shariah ndi Sunnah ndi malangizo ake owona mtima kwa mfumu.
za m’mene ayenera kuyendetsera zinthu za Khilafah Kunena zoona, Haarun Rashid (rahimahullah) adachitira umboni kuti Fudhail (rahimahullah) anali chitsanzo cha Sunnah.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu