Abdullah bin Abbaas (radhwiyallau ‘anhuma) Aa Alendo

Abaan bin Uthmaan (rahimahullah) akufotokoza kuti:

Tsiku lina, munthu wina anakonza zoti amuzunze Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) ndikumuchititsa manyazi. Anapita kwa atsogoleri onse achi Quraish nawauza kuti Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) akuwaitanira chakudya m’mawa otsatira. Munthuyo anapita malo osiyanasiyana ndipo anapitiriza kuitana anthu m’malo mwa Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma).

Tsiku lotsatira, nthawi ya chakudyacho, anthu ambiri anasonkhana m’nyumba ya Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma), yemwe atadziwa zoona zake za nkhaniyi, anapempha anthu kuti akhale pansi, anakagura zipatso kumsika ndipo anawaitana kuti adye. Ibnu Abbaas (radhiyallahu ‘anhuma) atakhala nawo ndikuyamba kulankhula nawo, ophika ambiri anayamba kukonza chakudya cha alendowo.

Anali akudyabe zipatsozo pamene chakudyacho chinkakonzedwa ndipo anapatsidwa. Alendo onse atadya mokwanira, Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) anafunsa msungichuma wake kuti, “Kodi tingathe kukonza chakudya choterechi kwa anthu tsiku lililonse?” Msungichumayo atanena kuti ndizotheka Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) anauza anthuwo kuti, “Nonsenu mukuitanidwa kudzadya chakudya chotere ndi ine m’mawa uliwonse.”

Zindikirani:

Nkhaniyi inachitika nthawi imene Maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) anali atapambana nkhondo zambiri (ndipo chuma cha dziko lapansi chinali m’manja mwawo). Komabe, Maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) anagwiritsa ntchito ndalama zambiri moti sanasunge chilichonse. Kukamba za chuma, zinali ngati ma sefa – madzi akathiridwa mu sefa, nthawi yomweyo amatuluka osatsala.

Swahaabi mmodzi ankapeza chuma chambiri, kudzera mukugonjetsa adani, koma kenako ankagwiritsa ntchito zonse zomwe apeza, ndipo sankasunga ngakhale dirham imodzi ngati yachakudya.

Analibe chizolowezi chosunga ndalama, kapena kutsogoza chilichonse pa zosowa zawo zamtsogolo. Ma dirham mazana ambiri, gawo lawo la zofunkha, ankagwiritsidwa ntchito mphindi zochepa.

(Fazaa’il-e-Sadaqaat pg. 705)

Check Also

kuzindikira kwakukulu kwa Abdullah bin Abbaas (radhiwyallahu ‘anhuma)

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) akuti: Mtumiki wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam) atamwalira, ndinauza …