Kuikonzekera Ramadhan

8. Pamene Ramadhan ikubwera komanso tili mkati kati mwa Ramadhan yesetsani kumanena dua yotsatirayi:

اَللّٰهُمَّ سَلِّمْنِيْ لِرَمَضَانَ وَسَلِّمْ رَمَضَانَ لِيْ وَسَلِّمْهُ لِيْ مُتَقَبَّلًا

O Allaah nditetezeni ine pondifikitsa m’mwezi wa Ramadhan (ndili wa thanzi komanso nyonga ndicholinga choti ndipindule kwambiri m’mweziwu) komanso usamaleni mwezi wa Ramadhan kwa ine (poupangitsa kuti ndikwanitse kupeza ma phindu ake ochuluka) komanso ndirandileni ine kusala kwanga.

عن عبادة بن الصامت قال كان رسول الله صلى الله عليه وسلم يعلمنا هؤلاء الكلمات إذا جاء رمضان اللهم سلمني لرمضان وسلم رمضان لي وسلمه لي متقبلا (الدعاء للطبراني، الرقم: 913)

Sayyiduna Ubaadah bin Saamit (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankatiphunzitsa ife mawu otsatirawa kumayambiliro kwa Ramadhan

اَللّهُمَّ سَلِّمْنِيْ لِرَمَضَان وَ سَلِّمْ رَمَضَانَ لِيْ وَسَلِّمْهُ لِيْ مُتَقَبَّلًا

9. Khalani ndi chizolowezi chopanga zinthu zabwino mu Ramadhan komanso ndi kusiya kupanga zoipa zonse

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا كان أول ليلة من شهر رمضان صفدت الشياطين ومردة الجن وغلقت أبواب النار فلم يفتح منها باب وفتحت أبواب الجنة فلم يغلق منها باب وينادي مناد يا باغي الخير أقبل ويا باغي الشر أقصر ولله عتقاء من النار وذلك كل ليلة (سنن الترمذي، الرقم: 682)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti mtumiki (salallah alayhi wasallama) anati usiku oyambilila wa mwezi wa Ramadhan ukangofika asatana onse ndi ziwanda zoipa zonse zimamangidwa, makomo onse a ku jahannam amatsekedwa moti palibe khomo ngakhale ndi limodzi lomwe limatsekulidwa, makomo onse a ku jannah amatsekulidwa moti palibe khomo olo ndi limodzi lomwe limatsekedwa ndipo olengeza amalengeza kuti: O iwe amene ukusaka saka zabwino yandikira! O iwe amene ukupanga zoipa chepetsa ndipo Allaah Ta’ala amapulumutsa mizimu yochuluka kuchokera ku moto usiku ulionse ndipo izi zimachitika mu Ramadhan yonse.

10. Ngati ungakwanitse kupereka chakudya cha iftaar (chomasulira swaumu) kwa munthu amene akusala ukhoza kutero, ngakhale utapereka chinthu chochepa ngati tende kuti amasulire swaumu yakeyo.

عن زيد بن خالد الجهني قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من فطر صائما كان له مثل أجره غير أنه لا ينقص من أجر الصائم شيئا (سنن الترمذي، الرقم: 807، وقال: هذا حديث حسن صحيح)

Sayyiduna Zaid bin khaalid Al-juhani (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti; Mtumiki wa Mulungu (salallah alayhi wasallama) adati; ´´Amene angamupase iftaar (chakudya chomasulira swaum) munthu amene akumanga swaum, Opatsayo adzalandila malipilo ofanana (ngati amunthu omangayo) popandanso kupunguka malipilo amunthu omangayo ngakhale pang´ono pomwe.

11. Onongerani nthawi yanu pokhala limodzi ndi anthu olungama pamene mukusala (talikilanani ndi anthu ochita zoipa).

12. Chitalikireni chinthu chilichonse chomwe chili cha Haraam komanso pewani zinthu zokayikitsa kuyambira zakudya, zakumwa, zintchito, zoyankhula ndi zina zotero.

13. Kumanga swaum m’mwezi wa Ramadan ndi Ibaada Yaikulu kwambiri (yokhala ndi malipilo ochuluka) choncho Munthu omanga Ramadan awonetsetse kuti akupewa zintchito zauchimo zimene zingapangitse kuluzika kwa malipiro akumangako. Chimodzimodzinso munthu omanga Ramadan azitalikitse ku m’chitidwe oyankhula zinthu zopanda pake (zolaula ndi zina zotere)

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه و سلم رب صائم ليس له من صيامه إلا الجوع ورب قائم ليس له من قيامه إلا السهر (سنن ابن ماجة، الرقم: 1690)

Sayyiduna Abu Hurayrah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti; Mtumiki wa Mulungu (sallallahu alaih wasallam) adati “Anthu ochuluka amamanga Ramadan komano samapeza malipiro mukumanga kwawo kupatula njala ndiponso ndi ochuluka mwa anthu amene amadzuka kupemphera swalat usiku koma samapeza malipilo aliwonse kungopatula kukhala osagona basi (kuvutika ndi tulo opanda malipiro)

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال : قال رسول الله صلى الله عليه وسلم : من لم يدع قول الزور والعمل به فليس لله حاجة في أن يدع طعامه وشرابه (صحيح البخاري، الرقم: 1903)

Sayyiduna Abu Hurayrah (radiyallah anhu) akusimba kuti, Mtumiki wa Mulungu (salallah alayhi wasallama) adati ´´Aliyense amene sakupewa kuyankhula zolaula (kutukwana, mabodza etc.) komanso amene sakupewa ntchito zoyalutsa (pamene akumanga) Allah alibe nawo ntchito kuziletsa kwake kudya ndikumwa (kusonyeza kuti munthu amemeyo alibe malipilo kwa Allah akungozivutitsa)

14. Pamene mukumanga Ramadan, Pewani kukangana ndikutukwanizana ndi anthu. Ngati munthu wina akufuna kukangana ndi inu amene mukumanga ramazani muwuzeni mwaulemu kuti inu mukusala.

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال : قال رسول الله صلى الله عليه وسلم : وإذا كان يوم صوم أحدكم فلا يرفث ولا يصخب فإن سابه أحد أو قاتله فليقل إني امرؤ صائم (صحيح البخاري، الرقم: 1904)

Sayyiduna Abu Hurayrah (radiyallah anhu) adati, Mtumiki wa Mulungu (salallah alayhi wasallama) adati; Pamene m’modzi wa inu ali Kumanga Ramadan asayankhule mawu oipa komanso asakalipe ndikupsa mtima. Ngati wina wake akutukwanani kapena akufuna kumenyana nanu (muuzeni mwaulemu kuti) Ine ndikumanga ramazani)

Check Also

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa …