عن عمر بن الخطاب رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: أكثروا الصلاة علي في الليلة الزهراء واليوم الأزهر فإن صلاتكم تعرض علي فأدعو لكم وأستغفر (القربة لابن بشكوال، الرقم: ١٠٧، وسنده ضعيف كما في المقاصد الحسنة، الرقم: ١٤٨)
Sayyiduna Umar bin Khattwaab (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Chulukitsani kundiwerengera Durood usiku ndi Usana wa tsiku la Jumuah (lachisanu) chifukwa Durood yanuyo imandipeza ndipo ndimakupangirani duwa kukupempherani chikhululuko kwa Allah ku machimo anu.
Kutsogoza Anthu Oyandikana Ndi Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)
Imaam Maalik (rahimahullah) ankayamba kuphunzitsa kaye anthu omwe anali m’ma Hadeeth ndi ophunzira omwe ankakhala mu nzinda wa Madina Tayyibah asadawaphunzitse anthu ena, atafunsidwa kuti ndi chifukwa chiyani akumasankha kaye kuphunzitsa hadith komanso anthu Okhala ku Madinah, iye adayankha kuti “awa ndi anthu omwe ndi oyandikirana ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). (Tarteeb-ul-Maadarik 13/2)