Zizindkiro za Qiyaamah 5

Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah pa nkhani ya Dajjaal

Kutulukira komanso kubwera kwa ma fitnah a Dajjaal zimayendera limodzi m’zitaab za Aqaa’id (Zikhulupiriro za Chisilamu). Ma Ulama a Aqaa’id amavomereza kuti kukhulupirira kutulukira kwa Dajjaal ndi gawo la Aqaa’id ya Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah.

Mahadith omwe mkati mwake Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adauchenjezeratu Ummah za ma fitnah a Dajjaal ndi ochuluka, kotero kuti zitaab za a Aqaa’id zonse aphatikiza kukhulupirira pa kubwera kwa Dajjaal kuti zikhale m’gulu la zikhulupiriro za Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah. Choncho, ma Muhadditheen akuluakulu adawaona kuti munthu amene angatsutse za kubwera kwa Dajjaal adzakhala m’gulu la opatuka monga Khawaarij, Mu’tazilah ndi ena otero.

Malinga ndi Allaamah Suyooti (Rahimahullah), ngati munthu angaitsutse hadith yomwe ikutsimikizira kupezeka kwa Dajjaal, adzakhala kafiri. Izi zatsimikizika mu Hadith ya Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam):

من كذب بالدجال فقد كفر ومن كذب بالمهدي فقد كفر

Amene angatsutse za Dajjaal wachita ukafiri, ndipo amene angatsutse za Mahdi (Radhwiya Allaahu ‘anhu) wachita ukafiri. (Al-Qowl-ul-Mukhtasar tsamba 16)

Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah ndikuti Dajjaal ndi Munthu Odziwika.

Ma Muhaddith komanso Fuqaha otchuka, Allaamah Qaadhwi Iyaaz (Rahimahullah), wanena momveka bwino kuti chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah ndikuti Dajjaal ndi munthu wina wake. Allaamah Qaadhi Iyaaz (Rahimahullah) wanena kuti:

Mahadith awa omwe Imaam Muslim (Rahimahullah) adafotokoza za Dajjaal ndi umboni kwa amene ali panjira ya Haq, kutsimikizira kukhalapo kwa Dajjaal ndikuti iye ndi munthu odziwika. Allah Ta’ala adzamtumiza kukhala mayesero kwa akapolo a Allah Ta’ala ndi kumpatsa mphamvu zochitira zinthu zina za uzimu, monga kuukitsa akufa amene adamupha, kutulutsa zinthu zokongora padziko lapansi. ndi kumeretsa nthaka youma yokhala ndi zinthu zabwino, ndi chilango, ndi mitsinje (yomwe azidzaiyendetsa), adzapangitsa chuma cha m’nthaka kumutsatira kulikonse, Kulamula mitambo kuti igwetse mvula, ndi nthaka kuti imeretse mbewu. Zozizwitsa zonsezi zidzaonekera kudzera mu mphamvu ya Allah Ta’ala ndi chilorezo Chake. Pambuyo pake, Allah Ta’ala adzathetsa mphamvu zake zonse, ndipo sadzatha kupha munthu (yemwe adamupha ndi kumuukitsa (monga momwe tafotokozera mu Hadith), kapena munthu wina aliyense. Nabiy Isa (‘alaihis salaam) adzamupha ndipo Allah Ta’ala adzadalitsa okhulupirira ndi kupirira pa Dini. Ichi ndi chikhulupiliro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah komanso ma Muhaddithiin onse, ma Fuqahaa ndi ma Ulama a Aqaa’id, mosiyana ndi amene akukanira za Dajjaal monga magulu osokera a Khawaarij, Jahmiyyah ndi ena mwa Mu’tazilah .

Check Also

Zizindikiro za Qiyaamah 1

Mma hadith odalitsika, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalosera zizindikiro zomwe zidzachitike Qiyaamah isanafike. Adauchenjeza …