Yearly Archives: 2022

Sayyiduna Abu Ubaidah (radhiyallahu) anhu aluza mano ake

Pankhondo ya Uhud Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adavulazidwa kwambiri ndi adani ndipo zitsulo za chipewa chake chodzitetezera pa nkhondo zinabaya pankhope yake yolemekezeka. Sayyiduna Abu Bakr Siddiq komanso Abu Ubaidah (Radhiyallahu anhuma) adathamangira kukamuthandizira Rasulullah (sallallahu alaih wasallam). Sayyiduna abu Ubaidah (radhiyallahu anhu) atafika pamene panali Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) …

Read More »

Tafseer Ya Surah Humazah

Tsoka kwa aliyense ochita miseche, wonyoza, wodziunjikira chuma ndikuchiwerengera! Akuganiza kuti chuma chake chidzamkhazika muyaya. Ayi! Ndithu, adzaponyedwa ku Hutwamah (kumoto waukali). Ndipo nchiyani chingakudziwitse kuti 'Hutamah' ndi chiyani? Ndi moto wa Allah woyatsidwa umene uzidzalowa m’mitima mwawo. (Motowo) udzatchingidwa ndi zipupa zitalizitali, ndi mizati yotambasulidwa (yotambasuka).

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

31.  Kupatula kupita kumzikiti kukapemphera, ngati kuli mtsonkhano omwe ukupangidwira mumzikiti, mukuyenera kupanga niya kuti mukupita kumzikiti kukaphunzira za Dini. Ngati wina angakwanitse kuphunzitsa dini choncho akuyenera kupanga niya kuti akubwera kumzikiti kukaphunzitsa dini. عن أبي هريرة رضي الله عنه قال سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول من …

Read More »

Machimo a zaka 80 akhululukidwa, kulandira malipiro ochita ibaadah kwa zaka 80 kudzera mu kuwerenga Duruud

Hazrat Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki sallallahu (sallallahu alaih wasallam) adati: munthu amene angaswali Asr tsiku la Jumuah ndipo kenako ndikuyamba kuwerenga Duruud iyi kokwana ka 80 asadaimilire malo wakhalawo, amakhululukidwa machimo a zaka 80 ndiponso amalipidwa zabwino kukhala ngati wapanga ibaadah kwa zaka 80.

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

27. Khalani mwaulemu ndi modekha pamene muli mumzikiti musakhale moiwala kulemekezeka kwa mzikiti. Anthu ena pamene akudikilira swalah kuti ichitike amaseweretsa zovala zawo kapena kusoweretsa mafoni. Kumeneku ndikuphwanya kulemekezeka ndi ulemelero wa mnzikiti.[1] 28. Thandizirani poupanga mzikiti kuti ukhale waukhondo nthawi zonse.[2] عن أبي سعيد الخدري رضي الله عنه قال …

Read More »

Uthenga Wa Sayyiduna Sa’d (Radhwiyallahu Anhu) Kupita Kwa Asilamu Onse

Nkatikati mwa nkhondo ya Uhud, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafunsa, “kodi Sa’d Bin Rabee alikuti? Sindikudziwa m’mene alili. ’kenaka, m’modzi mwa masahabah adatumizidwa kuti akamuyang’ane Sa’d (radhwiyallahu anhu), adapita pa malo pomwe anthu ofera ku nkhondo adagonekedwa. Adaitana mokuwa uku akutchula dzina la Sa’d kuti mwina adakali moyo. malo ena …

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

26 Osaipitsira mumzikiti. mwachitsanzo kulavulira mumzikiti kapena kumina mumzikiti mpaka zoipazo maminawo kapena malovuwo mkugwera pansi munzikiti.[1] عن أبي ذر رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم عرضت علي أعمال أمتي حسنها وسيئها فوجدت في محاسن أعمالها الأذى يماط عن الطريق ووجدت في مساوئ أعمالها النخاعة …

Read More »

Chikondi cha olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu pa Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam)

Usiku umene Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ankasamuka kupita ku Madinah Munawwarah makafiri adazungulira nyumba yake ndicholinga choti amuphe. Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) asadasamuke adamuuza Ali (radhwiyallahu anhu) kuti akagone ku nyumba ya Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndicholinga choti makafiri aganize ngati Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adakali m’nyumba momwemo sadatuluke ndipo …

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

24. Sizili zoloredwa kumuchotsa munthu pamalo ake mumzikiti cholinga choti akhalepo wina.

Olemekezeka Ibnu Umar (radhwiyallah anhu) akunena kuti Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adaletsa kuchotsedwa munthu wina pamalo ake ndikuti mumthu wina akhale pamalo ake. Choncho anthu akhoze malo oti akhale munthu amene (wabwera kumeneyo ngati zili zotheka kumupangira maloko).

Read More »