عن ابن عمر رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم زينوا مجالسكم بالصلاة علي فإن صلاتكم علي نور لكم يوم القيامة (الفردوس بمأثور الخطاب، الرقم: ٣٣٣٠، وإسناده ضعيف كما في القول البديع صـ 278)
Sayyiduna Ibnu Umar (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati “Kongoletsani mkumano wanu pondiwerengera Durood ine (kundifunila zabwino ine) chifukwa patsiku lachiweruzo durood idzakhala chobweretsa kuwala kwanu.
Chikondi Chenicheni Cha Masahabah (radhiyallahu anhum) Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)
Pamene mgwirizano wa Hudayibiyah adali kukambirana, Urwa ibn Mas’ud (radhwiyallahu anhu) yemwe adali mthumwi ya ma Quraysh (nthawi imeneyi adali asadalowe chisilamu Urwa.)
Urwa (radhwiyallahu anhu) adali ndi mwayi okutha kuona chikhalidwe cha Masahabah (radiyallah anhum) pa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam). Pamene Urwa adabwelera kwa anthu ake makafiri adayankhula kwa iwo nati: “Ndakhala m’makhoti amafumu akuluakulu padziko lapansi komanso ndakhala m’makhoti anduna ngati mthumwi, Ndakhala Ndinakumanapo ndi mfumu yaikulu ya Pesya, ya ku Roma komanso mfumu yaikulu ya ku Abisiniya. Palibe mwa maiko amenewa kumene anthu ake adakhalapo moizungulira Mfumu yawo moiwonetsera ulemu kwambiri ngati ndaonera omutsatira Muhammad (masahabah) akuchitira, Pamene Muhammad (sallallahu alayhi wasallam) walavula malovu, Malovu ake odalitsika sakuloredwa kufika pansi, pokhapokha akutengedwa ndi munthu wina m’manja mwake napaka ku nkhope kwake ndi thupi lake (akuchita izi kufuna kutenga madalitso). Pamene Muhammad walamula chinthu, munthu aliyense ozungulira iye akufulumilira kuti achite chinthucho iyeyo. Pamene akupanga wudhu, masahabah ake akukanganirana kuti atenge madzi amene akugwa kuchokera mziwalo zake, choncho aliyense pamalopo amafunitsitsa kuti madziwo awapeze. Pamene Iye akuyankhula wina aliyense akukhala chete Kamba ka ulemu. Palibe aliyense amene akukweza maso ake kumuyang´anitsitsa Iye Kamba ka ulemu. (Saheeh Bukhari, Pg,2731)