Njira Ya Sunnah Yopangira Adhaana

4. Kupanga Adhaana ndimau okweza kwambiri.[1]

عن عبد الله بن زيد رضي الله عنه قال … فأخبرته بما رأيت فقال إنها لرؤيا حق إن شاء الله فقم مع بلال فألق عليه ما رأيت فليؤذن به فإنه أندى صوتا منك (سنن أبي داود، الرقم: 499)[2]

Sayyiduna Abdullah mwana wa Zaydu (radhiyallah anhu) akusimba kuti …… Kenako ndinamuuuza Mtumiki (sallallah alayhi wasallam zamaloto amene ndidalota (komanso kapangidwe ka adhaana kamene ndinaphunzitsidwira mmalotomo).Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adayankha nati; Ndithudi ndimaloto owona inshaa Allah, Pita kwa Bilaal radhiyallah anhu ukamphunzitse mawu aadhaana amene wamva mmaloto ako kuti naye adzipanga adhaana pogwiritsa ntchito mawu amenewa, Chifukwa choti Bilaliyo mawu ake ndiokwera kwambiri kuposa mawu ako.

عن عبد الرحمن بن عبد الله بن عبد الرحمن بن أبي صعصعة الأنصاري ثم المازني عن أبيه أنه أخبره أن أبا سعيد الخدري رضي الله عنه قال له إني أراك تحب الغنم والبادية فإذا كنت في غنمك أو باديتك فأذنت بالصلاة فارفع صوتك بالنداء فإنه لا يسمع مدى صوت المؤذن جن ولا إنس ولا شيء إلا شهد له يوم القيامة قال أبو سعيد رضي الله عنه سمعته من رسول الله صلى الله عليه وسلم (صحيح البخاري، الرقم: 609)

Ndipo zasimbidwa kuchokera Kwa olemekezeka Abdullah bin Abdulrahmaan ibn Abi sa`sa`ah (radhiyallah anhu), iye akuti, nthawi ina olemekezeka Abu saidi khudriy (radhiyallah anhu) adati kwa iye, Ndikukuona kuti nthawi zonse umakhala koweta ziweto zako kutchire. Pamene iweyo uli kudyesa ziweto zako kapena uli kutchire (ndipo nthawi ya swalah ndikukhala kuti yakwana) ndipo ukufuna kuti upange adhaana, Choncho ukuyenera kukweza mawu ako popanga adhaana, Ndithudi kuyambira ziwanda, anthu ndicholengedwa chirichonse chimene chingamve mau amuadhini kuli konse mawuwo komwe akafikire, zolengedwazi zimenezo zidzamuchitira umboni (muadhiniyo) patsiku lachiweruzo”.Choncho olemekezeka Abuu Saeed (radhiyallah anhu) adati; Ndidamumva zimenezi Mtumiki (sallallah alayhi wasallam).

5. Kupanga azaana uli ndi wuzu.[3]

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال لا يؤذن إلا متوضئ (سنن الترمذي، الرقم: 200)[4]

Olemekedzeka Abuu Hurayrah radiyallah anhu akusimba kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallam a) adati; “Amene akupanga adhaana akuyenera kukhala ndi wuzu.


[1] أما حكم المسألة فإن كان يؤذن لجماعة استحب أن يرفع صوته ما أمكنه بحيث لا يلحقه ضرر (المجموع شرح المهذب 3/84)

[2] هذا الحديث سكت عنه أبو داود والمنذري (مختصر سنن أبي داود ١/٢٠٢)

[3] وأما آدابه فيستحب أن يكون متطهرا (روضة الطالبين 1/313)

[4] قال أبو هريرة رضي الله عنه لا ينادي بالصلاة إلا متوضئ قال أبو عيسى وهذا أصح من الحديث الأول قال أبو عيسى وحديث أبي هريرة لم يرفعه ابن وهب وهو أصح من حديث الوليد بن مسلم والزهري لم يسمع من أبي هريرة (سنن الترمذي، الرقم: 201)

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …