Tafseer Ya Surah Teen

وَالتِّينِ وَالزَّيْتُونِ ﴿١﴾ وَطُورِ سِينِينَ ﴿٢﴾ وَهَـٰذَا الْبَلَدِ الْأَمِينِ ﴿٣﴾ لَقَدْ خَلَقْنَا الْإِنسَانَ فِي أَحْسَنِ تَقْوِيمٍ ﴿٤﴾ ثُمَّ رَدَدْنَاهُ أَسْفَلَ سَافِلِينَ ﴿٥﴾ إِلَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَلَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍ ﴿٦﴾ فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعْدُ بِالدِّينِ ﴿٧﴾ أَلَيْسَ اللّٰـهُ بِاَحْكَمِ الْحَاكِمِينَ ﴿٨﴾

Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona, ndikulumbiliranso phiri la Sinai, ndikulumbiliranso Mzinda umenewu wa mtendere, ndithudi tamulenga munthu nkalengedwe kabwino ndi kolingana, ndipo kenako Tam’bweza kukhala wapansi kuposa a pansi, kupatula okhawo omwe akhulupilira ndikumachita ntchito zabwino, Iwo adzakhala nawo malipiro osatha. Tsono chikukuchititsa ndi chani kuti udzikanira za tsiku lachiweluzo. Kodi Allah simuweluzi wa nzeru mwa aweruzi onse.

وَالتِّينِ وَالزَّيْتُونِ ﴿١﴾ وَطُورِ سِينِينَ ﴿٢﴾وَهَـٰذَا الْبَلَدِ الْأَمِينِ

Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona ndiponso phiri la Sinai ndikulumbiliranso Mzinda uwu omwe ndi wa mtendere.

Mma Aya amenewa Allah akulumbilira malo okwana anayi omwe ndi olemekezeka pa dziko lino lapansi, malo amenewa ndi odalitsika kwabasi ndiponso mu nthawi inayake adali malo opezerapo chiongoko kwa aneneri angapo.

Mkuyu ndi Zitona zatchuridwazi zikuimira dziko la Palisitina ndi Siriya,malo omwe zipatso zimenezi zimabalana kwambiri, komanso ndi malo omwe Aneneri ambiri adakalarikira Dini ya Allah, Palisitina mwapaderadera ndi malo amene kudabadwira Nabi Isah (alaihis salaam) komanso ndikomwe iye adafalitsa uthenga wa Allah.

Tur, phiri la Sinai pamene Nabi Musah (alaihis salaam) adalandilira bukhu la Taurah.

Mzinda umenewu omwe ndi wa mtendere, uwu ndi Mzinda odalitsika wa Makkah Mukarramah omwe kupha chinyama Mzinda umenewu ndikoletsedwa. Mzinda wa Makkah ndi odala ndipo ndi wa mtendere kuposa mizinda ina yonse yomwe ikupezeka pa dziko lino lapansi ndipo ndi malo omwe Mtumiki omaliza Muhammad (sallallah alaih wasallam) adabadwira ndiponso pa kwawo pomwe adakhala asadasamukire ku Madinah Munawwarah.

Kotero Mma Aya amenewa Allah wazilumbilira zinthu zimenezi potengera ulemelero ochuluka omwe zithuzi ziri nazo.

لَقَدْ خَلَقْنَا الْإِنسَانَ فِي أَحْسَنِ تَقْوِيمٍ ﴿٤﴾ ثُمَّ رَدَدْنَاهُ أَسْفَلَ سَافِلِينَ ﴿٥﴾ إِلَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَلَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍ ﴿٦﴾ فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعْدُ بِالدِّينِ ﴿٧﴾ أَلَيْسَ اللّٰـهُ بِاَحْكَمِ الْحَاكِمِينَ ﴿٨﴾

Ndithudi tamulenga munthu nkalengedwe kabwino ndi kolingana, ndipo kenaka tamtsitsa ndikukhala wapansi mwa a pansi onse, kupatula okhawo omwe adakhulupilira mwa Allah ndikumachita ntchito zabwino, iwo akapatsidwa malipiro ochuluka opanda malire, nankha chikukuchititsa ndi chani kuti udzikanira za tsiku lachiweluzo, kodi Allah Sali muweluzi wa chilungamo mwa aweruzi onse.

Pambuyo polumbilira maiko amenewa kokwana kanayi, Allah akupeleka uthenga omwe ukuchokera mukulumbilira zinthu zimeneziziwu. Allah akufotokoza kunena kuti “Ndithudi tamulenga munthu nkaumbidwe kabwino, mmawu ena titha kunena kuti munthu akuyenera kukhala oganiza kuti Allah adasankha malo awiriwa ndikukhala odalitsika padziko lonse lapansi, chimodzimodzinso Allah adamusankha munthu kukhala cholengedwa chomwe ndichodalitsika kuposa zolengedwa zonse komanso adamulenga munthuyo nkalengedwe kabwino.

Ngati munthu angadzichengete ndikumatsatira malamulo a Allah omwe iye adawavumbulutsa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) Allah adzamukweza kuposanso angelo, koma ngati angatailire ndikumakhala umoyo wake mophwanya malamulo a Allah ndiye kuti adzatsitsidwa ulemelero wake ndikukhala wapansi (onyozeka) .

Otambasura ena amafotokoza kuti mawu oti “nkalengedwe kabwino” omwe atchuridwa mu surayi akutanthauza maonekedwe a munthu m’mene adaumbiridwira komanso kaganizidwe ndizina monga mphamvu ya kunva, kuona ndizina kuti zimakhala nkaumbidwe kabwino makamaka pamene ali wachinyamata. Komano akamakalamba amayamba kuluza maonekedwe ndikumafooka kufikira mpakana amatheratu ndikubwelera ku umwana kuli kufooka kwa thupi. Kotero mu Aya imeneyi Allah akunena kuti ngakhale munthuyo nthawi imene ziwalo zake zimakhala zitafooka, nkhani ndiyoti amatengedwabe kuti ndi olemekezeka pa maso pa Allah ndipo ntchito zonse zabwino zimene ankachita padziko lino lapansi zizidzachulukanabe patsiku lachiweruzo.

 فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعْدُ بِالدِّينِ ﴿٧﴾ أَلَيْسَ اللّٰـهُ بِاَحْكَمِ الْحَاكِمِينَ ﴿٨﴾

Tsono nchiyani chingakuchititse kuti ukanire za tsiku kubwera kwa tsiku lachiweruzo?Kodi Allah simuweluzi wa nzeru mwa aweruzi onse?

Mma Aya a m’mbuyomu Allah Ta’ala wankumbutsa munthu kuti adamulenga mkalengedwe kabwino ndipo adamusiyanitsa ndi zilengedwe zina zonse, Allah Ta’ala akumuuza munthu kuti kupambana kwake komanso ulemelero wake wagona mu kukhala munthu oopa Allah ndikulemekeza malamulo ake pochita ntchito zabwino, koma ngati angakhale ndi moyo onyozera malamulo ake adzatsitsidwa ulemelero wake ndikukhala munthu onyozeka komanso wapansi kwambiri ndipo adzaluza ulemu wake pamaso pa Allah. Chimodzimodzinso Allah wamuuza munthu kuti pambuyo posangalala ndi chinyamata pamene uli ndi mphamvu adzayamba kukalamba pang’ono ndi pang’ono ndipo mphamvu zonse zidzatha. Pa chifukwa chimenechi akufunika kutengerapo phunziro pa nkhani imeneyi ndi kuzindikira kuti pambuyo pa moyo umene tilinawowu palinso umoyo wina omwe ndi wamuyaya.

Mu Ayah imeneyi Allah Tabaaraka wata’ala akumudziwitsa munthu za mathero ake. Kunena kuti idzafika nthawi yomwe adzagonekedwe m’manda ndikukaonekera pamaso pa Allah patsiku lachiweruzo. Allah akufotokoza mofunsa kunena kuti ” nankha ndi chani chingakuchititse iweyo kuti ukanire za tsiku lachiweluzo? “mu kuyankhula kwina titha kunena kuti pambuyo poti munthu wadutsa mnyengo zosiyanasiyana ndipo waona kusintha kwa moyo wake ndikuzindikira kuti tsiku linalake adzamwalira, ndichifukwa chiyani akukanira za umoyo umene ulinkudza?

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …