عن أنس بن مالك قال:قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي بلغتني صلاته وصليت عليه وكتبت له سوى ذلك عشر حسنات (المعجم الأوسط للطبراني، وسنده لا بأس به كما القول البديع صـ 239)
Olemekezeka Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankhula kuti: munthu amene angawerenge durood kamodzi duruduyo imandifika kudzera mwa angelo kuphatikiza pamenepo zabwino zokwana khumi (10) zimalembedwa m’bukhu lake.
Dzina la Muhammad (sallallahu alaih wasallam) lipezeka m’bukhu la Taurah
Allaamah Sakhaawi (rahimahullah) adalongosora kuti padali munthu wina wake ochimwa kwambiri mu nthawi ya Bani Israail, atamwalira anthu sadalabadire zamoyo za ntembo wake ndipo adangousiya pantetete kenaka Allah adavumbulutsa kwa Nabi Musah (alaih salaam) kuti oo Musah sambitsani ntembowi ndipo opemphelele popeza munthu ameneyo ndamukhulukukira machimo ake.
Musah (alaihis salaam) adafunsa kuti Ndichifukwa chani mwamukhululukira? Allah adayankha kuti, tsiku linalake ankawerenga bukhu la Taurah ndipo a tafika pomwe padalembedwa dzina la Muhammad adawerenga Durudu, pa chifukwa chimenechi nd idamukhululukira machimo ake.