Kuwerenga Duruud ka 1000 lachisanu

عن أنس بن مالك قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي في يوم الجمعة ألف مرة لم يمت حتى يرى مقعده من الجنة (أخرجه ابن شاهين بسند ضعيف كذا في القول البديع صـ 397)

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki swallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angandiwelengere Duruud ka 1000 lachisanu lirilonse sadzamwalira pokhapokha ataonetsedwa malo ku Jannah.

Sayyiduna Abdullah Bin Amr (radhwiyallah Anhuma) Awotcha Chovala Chake

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aasi (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti:

Tsiku lina, Tidali limodzi ndi Nabi (salallah alaih wasallama) paulendo. Ndinapita kukamuona Iye nditavala chovala cha mtundu wachikasu/Oranje. (Ndi haraam kwa mwamuna kuvala chovala chamtundu wa yelo komanso oranje). Nabi (sallallahu alaih wasallam) adandifunsa,´Ichi nchiyani wavalachi? Ndipo ndidazindikira kuti sadasangalatsidwe nako kuvala kwanga zovala zamtundu umenewo. Choncho, pamene ndidafika kunyumba ndidapeza moto ukuyaka ndipo ndinaponya chovala changacho pamoto.

Tsiku lotsatila, pameme ndidapita kwa Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) adandifunsa ´chili kuti chovala chija? ´pamene ndinamuuza zimene ndinachita nacho chovalacho, adati ´Udayenera kumupatsa m’modzi mwa amayi akunyumba kwako, chifukwa azimayi amaloredwa kuvala zovala zamtundu umene uja”.

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aasi (radhwiyallahu anhuma) adavutika m’maganizo kwambiri poona kuti Sayyiduna Rasulullah (salallah alaih wasallama) adali okhumudwa, Choncho iye sadachedwe kupeza njira yothanirana ndi chovala chimene chidapangitsa kuti Nabi (salallah alaih wasallama) akhumudwe.Komanso sadaganizire kupeza njira ina yogwiritsira ntchito chovalacho. Tikadakhala ngati ifeyo m’malo mwa iyeyo bwenzi titakhala ndimaganizo owilingula kapena tikadangochisunga chovalacho kapena apo tikadapeza njira ina yogwiritsira ntchito. (Sunan Abi Dawood #4066)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …