Tafseer Ya Surah Feel

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ

أَلَمْ تَرَ كَيْفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِأَصْحَابِ الْفِيلِ ‎﴿١﴾‏ أَلَمْ يَجْعَلْ كَيْدَهُمْ فِي تَضْلِيلٍ ‎﴿٢﴾‏ وَأَرْسَلَ عَلَيْهِمْ طَيْرًا أَبَابِيلَ ‎﴿٣﴾‏ تَرْمِيهِم بِحِجَارَةٍ مِّن سِجِّيلٍ ‎﴿٤﴾‏ فَجَعَلَهُمْ كَعَصْفٍ مَّأْكُولٍ ‎﴿٥﴾‏

Kodi siudaone momwe Mbuye wako adawachitira anthu a Njovu? Kodi sadawaononge chiwembu chawo? Ndipo adawatumizira magulu ambalame mmagulumagulu otsatizana, ndikumawagenda ndi miyala yamoto; ndipo adawachita kukhala ngati mmera otafunidwatafunidwa ndiye walavuridwa.

Nkhani ya anthu a Njovu inachitika pafupifupi masiku makumi asanu ndi asanu asanabadwe Mtumiki (swallallahu alaih wasallam). Surah yonse ya Qur’an Shareef yaperekedwa pazochitika izi, zomwe zalembedwa m’mabuku a Tafseer, Hadith ndi Seerah.

Nkhani ya anthu a Njovu inali chilengezo cha Allah ndi chisonyezo chanzeru chosonyeza kuyandikira kwa chidindo cha Aneneri, Mtumiki Womaliza, Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam). Chitetezo cha Mulungu chomwe chidaperekedwa kwa makuraishi chidangochitika chifukwa chakuti Mtumiki womaliza, yemwe anali pafupi kuponda pa dziko lapansi, amachokera ku fuko lomwelo (makuraishi). Kupanda kutero, pankhani ya chikhulupiriro cha chipembedzo, mafumu a ku Abyssinia ndi Yemen anali abwino kuposa makuraish a ku Makka Mukarramah, popeza iwo adali anthu a bul pomwe makuraishi adali opembedza mafano.

Mu’jizah and Irhaas

Zozizwitsa zomwe zimaonekera m’manja mwa Mneneri pambuyo popatsidwa ntchito ya uneneri zimatchedwa mu’jizah. Kumbali inayi, chochitika chodabwitsa chomwe chimachitika ndi Mtumiki asanakhale mneneri chimatchedwa irhaas. Momwemonso, chizindikiro chosonyeza kubwera kwa Nabii chimatchedwanso irhaas. Kwenikweni, mawu akuti irhaas amatanthauza maziko kapena chiyambi. Kotero, zochitika zodabwitsa zoterozo zinapanga maziko olengeza za kubwera kwa ulosi.

Kuukira kwa Abraha kwa anthu a ku Makkah Mukarramah ndi kuwonongedwa kwake kotsatira kunachitika m’mwezi wa Muharram asanabadwe olemekezeka Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam).

Nkhani mwachidule yokhuza anthu anjovu ili motere:

Abraha adali mtsogoleri wa ku Yemeni amene adasankhidwa ndi mfumu Najaashi (Negus).poona ma arabu kuti amayenda mtunda wautali kupita ku Makkah yolemekezeka kukapanga mapemphero a Hajj, Abraha adali ndi nsanje yaikulu.Choncho adaganiza zomanga tchalitchi chapamwamba kuposa chilichonse komanso chowoneka bwino kudzela mudzina lachikhirisitu.Cholinga chake komanso mtsogolo lake amafuna kuti achipange tchalitchi chakecho kukhala likulu lopangilako mapemphero a hajji mmalo mwa Ka’bah. Choncho adapitiliza ndi cholinga chakecho ndipo adamanga tchalitchi chokongola kudera lotchedwa San’aa, imene idali likulu la Yemeni.Ndipo adayamba kuwaletsa anthu aku Yemeni kuti asamapite ku Makkah yolemekezeka ndipo adawalamulira kuti achipange tchalichicho kukhala mlowa mmalo wa ka’bah imene idamangidwa monyozeka. Haafiz Ibnu Kathir (rahimahullah) akuyankhula kuti Abraha adapeza zikongoletsero zamtengo wapatali zosiyanasiyana kuti akongoletsere tchalitchicho kuchokera kunyumba yachifumu ya Bilqis.

Pamene nkhani ya kumangidwa kwa tchalitchi chatsopano idawafikira anthu amtundu wa ma arabu anakwiya kwambiri.Munthu wina ochokera mufuko la Kinaanah, adanyamuka ndi cholinga chokamuyalutsa Abraha. Adapita pafupi ndi tchalichicho nakachitira chimbuzi malo ozungulila tchalichicho.Ena amayankhula kuti ena mwa anyamata afuko la ma arabu adayatsa moto pafupi ndi tchalichicho.Mphepo yamphamvu idauluzira lawi lamoto kufikira pathabwa latchalitchilo kenako lidayaka moto.Mosakhalitsa Abraha atadziwa adali ndimkwiyo waukulu ndipo adalumbira zokaphwanya Ka’bah yolemekezeka ndikukaifafaniza.

Ndi cholinga chake choipachi anapitilira kulunjika ku Makkah Molemekezeka ndi asilikali ake amphamvu ndi ochititsa mantha okwana zikwi zisanu ndi chimodzi (60000). Asilikali a Abraha anali limodzi ndi gulu lanjovu zimene zinatumizidwa ndi Negus. Mkatikati mwaulendo waku Makkah,fuko lililonse lomwe linkayesera kuwatchingira pompopompo limagonjetsedwa ndi lupanga lamphamvu la Abraha. pamene asilikali a Abraha adakafika malo otchedwa Mughammas, pafupi ndi Makkah yolemekezeka ,Abraha adalamula kuti ziweto za anthu a ku Makkah zomwe zinkadya zilansidwe kudzera mu lamulo la Aswad Ibn Maqsud. Munyamazo mudali ngamila mazana awiri za Abdul Muttalib,agogo ake a Mtumiki Muhammad (swallallahu ‘alaihi wasallam). Abdul Muttalib adali mtsogoleri wa ma Quraish komanso wamkulu oyang´anira Ka’bah yolemekezeka. pamene adalandila maganizo Abraha amene anali ndi cholinga choipa , Abdul Muttalib adasonkhanitsa ma Quraish ndipo adawatsimikizira kuti asachite mantha.ndipo anawakumbutsa kuti Ka’bah yoyerayi ndi nyumba ya Allah Ta’ala ndipo kuti Mulunguyo popanda chikayiko nyumba yakeyo ayiteteza. Kenako adapereka malangizo kuti anthu onse achoke mtawuni ya Makkah.

Asadanyamuke,adakhala limodzi ndi ana ake komanso ndi ena ochepa mwa atsogoleri a Ma Quraysh, Abdul Muttalib adanyamuka ulendo okakumana ndi Abraha. Mosakhalitsa Abraha adaona Abdul Muttalib, adatsika pampando wake wachifumu ndipo adamuonetsera Abdul Muttalib kumulandila kwabwino ndipo anamulemekeza. Abdul Muttalib adali ongola kwambiri, kuwala komanso Okhala ndi maonekedwe owopsya komanso olwmekezeka. Munthu wina aliyense amene amakumana naye koyamba ankagwidwa ndi mantha chifukwa cha kulemekezeka kwake. Abrahanso zidamuchitikira chimodzimodzi mu kukumana koyamba.

Pambuyo potenga ngamila zake , Abdul Muttalib Ndipo adawalamula kuti achoke onse mmakkah. Kenako adalumbulila kuti apereka nsembe ngamila mazana awiri (200) popempha Allah kuti ateteze Ka’bah. Asadapite kuphiri , Abdul Muttalib adagwira khomo la Ka’bah napempha kwa Allah Ta’ala ndi mawu awa:

لاهُمّ أن المرء يمــنع … رحله فامنع رحالك

Ambuye Mulungu !munthu amateteza nyumba yake nanunso tetezani nyumba yanu.

وانصر على آل الصليــب … وعابديه اليوم آلك

Athandizeni anthu anu kulimbana ndi anthu a mtanda ndizomwe amapembedza.

لا يغلبن صليبهم … ومحالهم أبدًا محالك

Mitanda yawo komanso chiwembu chawo sizingapose mapulani anu inu Allah.

جروا جميع بلادهم … والفيل كي يسبوا عيالك

Atenga nabweretsa gulu la asilikali awo onse kudzaononga Ufumu wanu

عمدوا حماك بكيدهم … جهلًا وما رقبوا جلالك

Chifukwa chaumbuli ndikusazindikira iwo apanga chiwembu kuti aononge malo anu oyera (Haram) ndipo alephera kuganizira ukulu wanu inu Allah Taala.

Pamene adatsiriza duwa yake duwa yapansi pamtima, Abdul Muttalib pamodzi ndi a mnzake adakakwera phiri nasiya makkah mopanda kanthu komanso mulibe aliyense.

Mamawa wake otsatira Abraha adakhozekeretsa gulu lake la asilikali nakwera njovu yake yotchedwa Mahmood (Imeneyi idali mtsogoleri wanjovu zonse) kukhozekera kukamenya nkhondo. pamene amamuyang´anitsa Mahmood kulunjika ku Makkah Mukarramah, munthu wina otchedwa Nufail bin Habib ananong´oneza mmakutu a Mahamood , “Khala pansi Mahmood! bwerera kumene wachokera. iwe uli munthaka yoyeretsedwa!” kenako adasiya makutu akewo.Njovu ija pompopompo idavomereza ndipo idagwada pansi uku Nufail akuthamangira kupita kuphiri. Anthu adayamba kuyimenya njovu ija ndizikwapu zachitsulo komano siidasunthe. Ngati ikadayang´anitsidwa kulunjika ku Yemen kapena kumbali iliyonse, ndiye kuti ikadafulumira kupita, koma pamene ikuyang´anitsidwa kumakkah ikugwada pansi ndikukana kuyenda.

Pamene ankakhozekera kuti tsopano awononge ka’bah, mwadzidzidzi khwimbi lambalame zing´onozing´ono zidaonekera kuchokera kumbali yakunyanja, Mbalame iliyonse idanyamula timiyala titatu . Kamwala kali konse kamafanana kukula kwake ngati sawawa kapena Nandolo. Mbalame iliyonse idanyamula timiyala tiwiri muzala zake ndipo kamodzi kukamwa kwake. Mbalamezi zidaponyera timiyalati kwa Abrahah ndigulu la asilikali ake. Ndipo munthu aliyense woipa amene adagendedwa ndi timiyalato imfa imakhala yomweyo. Kamwala kalikonse kadayikidwa dzina la munthu amene adakhozeredwa kuti ukamugende komanso ndi dzina labambo ake. Kudzera mumphavu ya Allah timiyalati tinkagwa ngati mvula pa asilikali a Abraha ngati Zipolopolo ndi machaka. Kamwalako kamalasa mutu wamunthu kukatulukira kumbuyo kamba kamphavu yake. Asilikali komanso njovu zidayamba kuthawa, atapanikizidwa, ambiri mwa iwo adafa nthawi yomweyo pamene ena mwa iwo adafa ali paulendo wawo obwerera kwawo. Kudzera munjira imeneyi Abraha ndi gulu lake lamphamvu la asilikali lidaonongekeratu nilichotsedwa padziko pano.

Abraha, pambuyo poti walasidwa ndi timiyalato adakhudzidwa ndimatenda akupha amene adafalisa poizoni thupi lake lonse. pamene amkamuchotsa thupi lake lidali litatuluka mphere uku zikutulutsa mafinya ndi magazi. Mmodzimmodzi chiwalo cha aliyense chapathupi chimayoyoka ndikugwera pansi. Potsilizira pamene amakafika malo otchedwa San’aa, chidali chake chidaphulika namwalila pompo imfa yodandaulitsa.

Allah Ta’ala akuyankhula mu Quraan yolemekezeka:

أَلَمْ تَرَ كَيْفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِأَصْحَابِ الْفِيلِ ‎﴿١﴾‏ أَلَمْ يَجْعَلْ كَيْدَهُمْ فِي تَضْلِيلٍ ‎﴿٢﴾‏ وَأَرْسَلَ عَلَيْهِمْ طَيْرًا أَبَابِيلَ ‎﴿٣﴾‏ تَرْمِيهِم بِحِجَارَةٍ مِّن سِجِّيلٍ ‎﴿٤﴾‏ فَجَعَلَهُمْ كَعَصْفٍ مَّأْكُولٍ ‎﴿٥﴾‏

Zomwe taphunzira mu surayi

1) Nsanje ndi kaduka ndi matenda owononga. Zimayambitsa mikangano. Munthu amene ali ndi nsanje amakhala wokwiya nthawi zonse ndipo amafufuza njira zomuposa munthu wina. Nsanje ya Abraha ndi imene inam’pangitsa kumanga “mdani wa Ka’ba”, ndipo izi n’zimene zinamufikitsa ku chiwonongeko chake.

2) Mkwiyo umapangitsa kuti munthu asokonezeke maganizo, ndipo akapsa mtima amapanga zisankho zomwe pambuyo pake adzanong’oneza nazo bondo. Kotero, tikuona kuti chisankho cha Abraha chofuna kuwononga Ka’ba chinamtengera ku chionongeko ndipo chinamfikitsa ku mapeto ake omvetsa chisoni.

3) Ngati nkwiyo siuziziritdsidwa, munthu adzagwa m’mavuto aakulu. Abraha akadapanda kudzikuza, sakanakhala ndi nsanje ndikumanga nyumba yolimbana nayo. Zikanamupulumutsa ku mavuto ambiri.

4) Mphamvu ndi ulemelero zonse ndi za Allah Ta’ala. Allah Ta’ala yekha ndiye wamphamvu. Chilichonse chili m’manja mwake. Ngati afuna, adzawononga njovu zazikulu ndi timiyala tating’ono. Choncho, munthu sakuyenera kuchita mantha ndi mphamvu za dziko. Ngati Allah Ta’ala amuteteza munthu, palibe amene angamupweteke ngakhale ali ndi mphamvu ndi ulemerelo.

5) Allah Ta’ala amatumiza chithandizo Chake kwa amene akudzipereka kwa Iye ndi mtima wonse.

6) Mtetezi ndi Myang’aniri wa Deen ndi Allah Taala. Adzagwiritsa ntchito amene wafuna ndi chilichonse chimene wafuna kuti atetezere Deen. Choncho potumikira Deen, munthu asachite chilichonse choletsedwa ndi chimene chingamkwiyitse Allah Taala.

7) Tizikumbukira nthawi zonse kuti Allah Ta’ala sadalira khama lathu poteteza Chisilamu. Choncho, titengere njira za Halaal zomwe Allah Ta’ala watilamula kuzitenga ndipo pambuyo pake titsamire kwa Allah Ta’ala kuti abweretse zotsatira zabwino.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …